Luka 8:47 - Buku Lopatulika47 Ndipo mkaziyo pakuona kuti sanabisike, anadza ndi kunthunthumira, nagwa pamaso pake, nafotokoza pamaso pa anthu onsewo chifukwa chake cha kumkhudza Iye, ndi kuti anachiritsidwa pomwepo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201447 Ndipo mkaziyo pakuona kuti sanabisike, anadza ndi kunthunthumira, nagwa pamaso pake, nafotokoza pamaso pa anthu onsewo chifukwa chake cha kumkhudza Iye, ndi kuti anachiritsidwa pomwepo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa47 Pamene mai uja adaona kuti sangathenso kudzibisa, adadza monjenjemera nadzigwetsa ku mapazi a Yesu. Adafotokoza pamaso pa anthu onse aja chifukwa chimene adaakhudzira Yesu, ndiponso m'mene adachirira nthaŵi yomweyo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero47 Ndipo mayiyo podziwa kuti sanathe kuchoka wosadziwika, anabwera akunjenjemera ndipo anagwa pa mapazi a Yesu. Pamaso pa anthu onse, anafotokoza chifukwa chimene anamukhudzira Iye ndi mmene iye anachiritsidwira nthawi yomweyo. Onani mutuwo |