Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 8:39 - Buku Lopatulika

39 Pita kunyumba kwako, nufotokozere zazikuluzo anakuchitira iwe Mulungu. Ndipo iye anachoka, nalalikira kumzinda wonse zazikuluzo Yesu anamchitira iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

39 Pita kunyumba kwako, nufotokozere zazikuluzo anakuchitira iwe Mulungu. Ndipo iye anachoka, nalalikira kumudzi wonse zazikuluzo Yesu anamchitira iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

39 “Iyai, iwe bwerera kwanu, ukafotokoze zazikulu zimene Mulungu wakuchitira.” Munthuyo adapitadi kwao nkumakalengeza mumzinda monse zazikulu zimene Yesu adaamchitira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

39 “Bwerera kwanu kafotokoze zimene Mulungu wakuchitira.” Ndipo munthuyo anachoka ndi kukanena ku mzinda wonsewo zimene Yesu anamuchitira iye.

Onani mutuwo Koperani




Luka 8:39
13 Mawu Ofanana  

Idzani, imvani, inu nonse akuopa Mulungu, ndipo ndidzafotokozera zonse anazichitira moyo wanga.


Koma iye anatuluka nayamba kulalikira ndithu, ndi kubukitsa mauwo, kotero kuti Yesu sanathe kulowanso poyera m'mudzi, koma anakhala padera m'mapululu; ndipo anadza kwa Iye anthu a kumalo onse.


Ndipo m'mene Iye analikulowa mungalawa, anampempha waziwanda uja kuti akhale ndi Iye.


Ndipo sanamlole, koma ananena naye, Muka kwanu kwa abale ako, nuwauze zinthu zazikulu anakuchitira Ambuye, ndi kuti anakuchitira chifundo.


Ndipo munthuyo amene ziwanda zinatuluka mwa iye anampempha Iye akhale ndi Iye; koma anamuuza apite, nanena,


Ndipo pakubwera Yesu, khamu la anthu linamlandira Iye; pakuti onse analikumlindira Iye.


Tiyeni, mukaone munthu, amene anandiuza zinthu zilizonse ndinazichita: ameneyu sali Khristu nanga?


Iye ndiye lemekezo lanu, Iye ndiye Mulungu wanu, amene anachita nanu zazikulu ndi zoopsa izi, mudaziona m'maso mwanu.


Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m'banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupirira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa