Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 7:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo Yesu anapita nao. Ndipo pakufika Iye tsono pafupi pa nyumba yake, kenturiyo anatuma kwa Iye abwenzi ake, kunena naye, Ambuye, musadzivute; pakuti sindiyenera ine kuti mudzalowe pansi pa tsindwi langa;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo Yesu anapita nao. Ndipo pakufika Iye tsono pafupi panyumba yake, kenturiyo anatuma kwa Iye abwenzi ake, kunena naye, Ambuye, musadzivute; pakuti sindiyenera ine kuti mudzalowe pansi pa chindwi langa;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Tsono Yesu adapita nawo. Pamene Iye ankayandikira nyumba yake, mkulu wa asilikali uja adatuma abwenzi ake kwa Yesu kukamuuza kuti, “Ambuye, musadzivute, pakuti sindili woyenera kuti Inu nkuloŵa m'nyumba mwanga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Pamenepo Yesu anapita nawo. Iye sanali patali ndi nyumba pamene Kenturiyo anatumiza anzake kuti akamuwuze kuti, “Ambuye, musadzivutitse, pakuti ndine wosayenera kuti mulowe mʼnyumba mwanga.

Onani mutuwo Koperani




Luka 7:6
15 Mawu Ofanana  

sindiyenera zazing'ono za zifundo zonse, ndi zoona zonse, zimene mwamchitira kapolo wanu: chifukwa ndindodo yanga ndinaoloka pa Yordani uyu; ndipo tsopano ndili makamu awiri.


Kudzikuza kwa munthu kudzamchepetsa; koma wokhala ndi mtima wodzichepetsa adzalemekezedwa.


monga Mwana wa Munthu sanadze kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.


Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima; koma Iye wakudza pambuyo panga, ali wakundiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake: Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:


Ndipo ananka naye pamodzi; ndipo khamu lalikulu linamtsata Iye, ndi kumkanikiza Iye.


Koma Simoni Petro, pamene anaona, anagwa pansi pa mawondo ake a Yesu, nanena, Muchoke kwa ine, Ambuye, chifukwa ndine munthu wochimwa.


Ndipo iwo, pakufika kwa Yesu, anampempha Iye koumirira, nati, Ayenera iye kuti mumchitire ichi;


pakuti akonda mtundu wathu, ndipo anatimangira ife sunagoge.


chifukwa chake ine sindinadziyesera ndekha woyenera kudza kwa Inu: koma nenani mau, ndipo mnyamata wanga adzachiritsidwa.


M'mene Iye anali chilankhulire, anadza wina wochokera kwa mkulu wa sunagoge, nanena, Mwana wako wafa; usamvute Mphunzitsi.


za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu anamdzoza Iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse osautsidwa ndi mdierekezi, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi Iye.


Dzichepetseni pamaso pa Ambuye, ndipo adzakukwezani.


Koma apatsa chisomo choposa. Potero anena malembo, Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo odzichepetsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa