ndi zakudya za pa gome lake, ndi makhalidwe a anyamata ake, ndi maimiriridwe a atumiki ake, ndi zovala zao, ndi otenga zikho ake, ndi nsembe yake yopsereza imene amapereka m'nyumba ya Yehova, anakhululuka malungo.
chaka chachitatu cha ufumu wake, anakonzera madyerero akalonga ake onse, ndi omtumikira; amphamvu a Persiya ndi Mediya, omveka ndi akalonga a maikowo anakhala pamaso pake,
Ndipo kunali tsiku lachitatu, Estere anavala zovala zake zachifumu, nakaimirira m'bwalo la m'kati la nyumba ya mfumu, popenyana pa nyumba ya mfumu; ndi mfumu inakhala pa mpando wake wachifumu m'nyumba yachifumu, pandunji polowera m'nyumba.
Ndipo Mordekai anatuluka pamaso pa mfumu wovala chovala chachifumu chamadzi ndi choyera, ndi korona wamkulu wagolide, ndi malaya abafuta ndi ofiirira; ndi mzinda wa Susa unafuula ndi kukondwera.
Ndipo Yohane yekhayo anali nacho chovala chake cha ubweya wangamira, ndi lamba lachikopa m'chuuno mwake; ndi chakudya chake chinali dzombe ndi uchi wakuthengo.
Ndipo atachoka amithenga ake a Yohane, Iye anayamba kunena za Yohane kwa anthu a makamu aja, nati, Munatuluka kunka kuchipululu kukapenya chiyani? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi?