Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 7:24 - Buku Lopatulika

24 Ndipo atachoka amithenga ake a Yohane, Iye anayamba kunena za Yohane kwa anthu a makamu aja, nati, Munatuluka kunka kuchipululu kukapenya chiyani? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Ndipo atachoka amithenga ake a Yohane, Iye anayamba kunena za Yohane kwa anthu a makamu aja, nati, Munatuluka kunka kuchipululu kukapenya chiyani? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Amithenga a Yohane aja atachoka, Yesu adayamba kufunsa makamu a anthu aja za Yohane kuti, “Kodi m'mene mudaapita ku chipululu, mudaati mukaona chiyani? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Anthu otumidwa ndi Yohane aja atachoka, Yesu anayamba kuyankhula ndi gulu la anthu za Yohaneyo kuti, “Kodi munkapita ku chipululu kukaona chiyani? Bango logwedezeka ndi mphepo?

Onani mutuwo Koperani




Luka 7:24
14 Mawu Ofanana  

Wobwabwada ngati madzi; sudzapambana; chifukwa unakwera pa kama wa atate wako; pamenepo unaipitsapo; anakwera paja ndigonapo.


Ndipo mwanayo anakula, nalimbika mu mzimu wake, ndipo iye anali m'mapululu, kufikira masiku akudzionetsa yekha kwa Israele.


pa ukulu wansembe wao wa Anasi ndi Kayafa, panadza mau a Mulungu kwa Yohane mwana wa Zekariya m'chipululu.


Ndipo wodala iye amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.


Koma munatuluka kukaona chiyani? Munthu wovala zovala zofewa kodi? Onani, iwo akuvala zolemera, ndi akukhala odyerera, ali m'nyumba za mafumu.


Anati, Ndine mau a wofuula m'chipululu, Lungamitsani njira ya Mbuye, monga anati Yesaya mneneriyo.


Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusocheretsa;


Aphunzitsi onamawo ndiwo akasupe opanda madzi, nkhungu yokankhika ndi mkuntho; amene mdima wakuda bii uwasungikira.


Inu, tsono, okondedwa, pozizindikiratu izi, chenjerani, kuti potengedwa ndi kulakwa kwa iwo osaweruzika, mungagwe kusiya chikhazikiko chanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa