Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 7:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo anayandikira, nakhudza chithatha; ndipo akumnyamulawo anaima. Ndipo Iye anati, Mnyamata iwe, ndinena ndi iwe, Tauka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo anayandikira, nakhudza chithatha; ndipo akumnyamulawo anaima. Ndipo Iye anati, Mnyamata iwe, ndinena ndi iwe, Tauka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Tsono adafika pafupi nakhudza chithathacho. Anthu amene ankanyamula malirowo adaima, ndipo Yesu adati, “Mnyamata iwe, ndikukuuza kuti, Uka.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Kenaka anapita nakakhudza chithatha cha maliro ndipo amene anachinyamulawo anayima. Iye anati, “Mnyamata, ndikukuwuza kuti, dzuka!”

Onani mutuwo Koperani




Luka 7:14
20 Mawu Ofanana  

Nafungatira katatu pa mwanayo, nafuulira kwa Yehova, nati, Yehova Mulungu wanga, ndikupemphani, ubwere moyo wake wa mwanayu m'chifuwa mwake.


Ndipo Yehova anamva mau a Eliya, ndipo moyo wa mwanayo unalowanso mwa iye, nakhalanso moyo.


momwemo munthu agona pansi, osaukanso; kufikira miyamba kulibe, sadzaukanso, kapena kuutsidwa pa tulo take.


Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi? Ndikadayembekeza masiku onse a nkhondo yanga, mpaka kwafika kusandulika kwanga.


Pakuti ananena, ndipo chinachitidwa; analamulira, ndipo chinakhazikika.


Akufa anu adzakhala ndi moyo; mitembo yao idzauka. Ukani muimbe, inu amene mukhala m'fumbi; chifukwa mame ako akunga mame a pamasamba, ndipo dziko lapansi lidzatulutsa mizimu.


Ndipo anagwira dzanja lake la mwana, nanena kwa iye, Talita koumi, ndiko kunena posandulika, Buthu, ndinena ndi iwe, Uka.


Ndipo pamene Ambuye anamuona, anagwidwa ndi chifundo chifukwa cha iye, nanena naye, Usalire.


Ndipo wakufayo anakhala tsonga, nayamba kulankhula. Ndipo anampereka kwa amake.


Ndipo mbiri yake imeneyo inabuka ku Yudeya yense, ndi ku dziko lonse loyandikira.


Yesu anati kwa iye, Ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo;


Pakuti monga Atate aukitsa akufa, nawapatsa moyo, momwemonso Mwana apatsa moyo iwo amene Iye afuna.


Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti ikudza nthawi, ndipo ilipo tsopano, imene akufa adzamva mau a Mulungu; ndipo iwo akumva adzakhala ndi moyo.


monga kwalembedwa: Ndinakukhazika iwe kholo la mitundu yambiri ya anthu pamaso pa Mulungu amene iye anamkhulupirira, amene apatsa akufa moyo, ndi kuitana zinthu zoti palibe, monga ngati zilipo.


pakuti zochitidwa nao m'tseri, kungakhale kuzinena kuchititsa manyazi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa