Luka 7:12 - Buku Lopatulika12 Ndipo pamene anayandikira kuchipata cha mzindawo, onani, anthu analikunyamula munthu wakufa, mwana wamwamuna mmodzi yekha, amake ndiye mkazi wamasiye; ndipo anthu ambiri amumzinda anali pamodzi naye. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201412 Ndipo pamene anayandikira kuchipata cha mudziwo, onani, anthu analikunyamula munthu wakufa, mwana wamwamuna mmodzi yekha, amake ndiye mkazi wamasiye; ndipo anthu ambiri akumudzi anali pamodzi naye. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa12 Pamene Yesu ankayandikira chipata cha mudziwo, adakumana ndi anthu atanyamula maliro. Womwalirayo anali mwana wamwamuna. Mai wake wa mwanayo anali wamasiye, ndipo mwana wake anali yekhayo. Anthu ambirimbiri am'mudzimo anali naye. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero12 Akufika pa chipata cha mudziwo, anakumana ndi anthu amene ankatuluka ndi munthu wakufa amene anali mwana yekhayo wa mkazi wamasiye. Gulu lalikulu la anthu a mʼmudziwo linali naye. Onani mutuwo |
Ndipo onani, chibale chonse chinaukira mdzakazi wanu, ndi kuti, Upereke iye amene anakantha mbale wake, kuti timuphe chifukwa cha moyo wa mbale wake amene anamupha; koma pakutero adzaononga wolowa yemwe; chomwecho adzazima khala langa lotsala, ndipo sadzasiyira mwamuna wanga dzina kapena mbeu kunja kuno.