Luka 6:42 - Buku Lopatulika42 Kapena ungathe bwanji kunena kwa mbale wako, Mbale iwe, leka ndichotse kachitsotso kali m'diso lako, wosayang'anira iwe mwini mtanda uli m'diso lako? Wonyenga iwe! Yamba wachotsa mtandawo m'diso lako, ndipo pomwepo udzayang'anitsa bwino kuchotsa kachitsotso ka m'diso la mbale wako. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201442 Kapena ungathe bwanji kunena kwa mbale wako, Mbale iwe, leka ndichotse kachitsotso kali m'diso lako, wosayang'anira iwe mwini mtanda uli m'diso lako? Wonyenga iwe! Thanga wachotsa mtandawo m'diso lako, ndipo pomwepo udzayang'anitsa bwino kuchotsa kachitsotso ka m'diso la mbale wako. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa42 Ungamuuze bwanji mbale wako kuti, ‘Mbale wanga, taima ntakuchotsa kachitsotso kali m'maso mwakoka,’ pamene iweyo sukuchiwona chimtengo chimene chili m'maso mwako momwe? Iwe wachiphamaso, yamba wachotsa chimtengo m'maso mwako, pamenepo ndiye udzatha kupenya bwino nkukachotsa kachitsotso kamene kali m'maso mwa mbale wako.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero42 Kodi munganene bwanji kwa mʼbale wanu kuti, ‘Mʼbale nʼtakuchotsa kachitsotso mʼdiso mwako,’ pamene inu eni ake mukulephera kuona mtengo uli mʼdiso mwanu? Inu achiphamaso, yambani mwachotsa mtengo uli mʼdiso mwanu, ndipo kenaka mudzaona bwinobwino ndi kuchotsa kachitsotso mʼdiso la mʼbale wanu.” Onani mutuwo |