Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 6:41 - Buku Lopatulika

41 Ndipo uyang'aniranji kachitsotso kali m'diso la mbale wako, koma mtanda wa m'diso la iwe mwini suuzindikira?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

41 Ndipo uyang'aniranji kachitsotso kali m'diso la mbale wako, koma mtanda wa m'diso la iwe mwini suuzindikira?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

41 “Umaoneranji kachitsotso kamene kali m'maso mwa mnzako, koma osaganizako za chimtengo chimene chili m'maso mwako momwe?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

41 “Kodi ndi chifukwa chiyani mumaona kachitsotso mʼdiso la mʼbale wanu ndi kusasamala mtengo uli mʼdiso mwanu?

Onani mutuwo Koperani




Luka 6:41
18 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova adzambwezera mwazi wake pamutu wake wa iye yekha, popeza iye anawakantha anthu awiri olungama ndi okoma oposa iye mwini, nawapha ndi lupanga, atate wanga Davide osadziwa, ndiwo Abinere mwana wa Nere kazembe wa khamu la nkhondo la Israele, ndi Amasa mwana wa Yetere kazembe wa khamu la nkhondo la Yuda.


Koma sanawerenge Alevi ndi Abenjamini pakati pao; pakuti mau a mfumu anamnyansira Yowabu.


Pakuti adzidyoletsa yekha m'kuona kwake, kuti anthu sadzachipeza choipa chake ndi kukwiya nacho.


Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika, ndani angathe kuudziwa?


Popeza anasamalira, natembenukira kuleka zolakwa zake zonse adazichita, adzakhala ndi moyo ndithu, sadzafa.


Musaweruze, kuti mungaweruzidwe.


Ndipo anali nato tinsomba towerengeka; ndipo Iye anatidalitsa, nati atipereke itonso.


Wophunzira saposa mphunzitsi wake; koma yense, m'mene atakonzedwa mtima, adzafanana ndi mphunzitsi wake.


Kapena ungathe bwanji kunena kwa mbale wako, Mbale iwe, leka ndichotse kachitsotso kali m'diso lako, wosayang'anira iwe mwini mtanda uli m'diso lako? Wonyenga iwe! Yamba wachotsa mtandawo m'diso lako, ndipo pomwepo udzayang'anitsa bwino kuchotsa kachitsotso ka m'diso la mbale wako.


Koma pamene anakhalakhala alikumfunsabe Iye, anaweramuka, nati kwa iwo, Amene mwa inu ali wopanda tchimo, ayambe kumponya mwala.


Chifukwa chake uli wopanda mau owiringula, munthu iwe, amene uli yense wakuweruza; pakuti m'mene uweruza wina, momwemo udzitsutsa iwe wekha, pakuti iwe wakuweruza, umachita zomwezo.


pakuti wadziyang'anira yekha, nachoka, naiwala pompaja nali wotani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa