Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 5:30 - Buku Lopatulika

30 Ndipo Afarisi ndi alembi ao anang'ung'udza kwa ophunzira ake, nanena, kuti, Bwanji inu mukudya ndi kumwa pamodzi ndi anthu amisonkho ndi ochimwa?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 Ndipo Afarisi ndi alembi ao anang'ung'udza kwa ophunzira ake, nanena, kuti, Bwanji inu mukudya ndi kumwa pamodzi ndi anthu amisonkho ndi ochimwa?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Afarisi pamodzi ndi aphunzitsi ao a Malamulo adayamba kuŵinya, nafunsa ophunzira ake kuti, “Bwanji mukudya ndi kumwa pamodzi ndi okhometsa msonkho, ndi anthu ochimwa?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 Koma Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo amene anali a gulu lawo anadandaula kwa ophunzira ake, “Kodi ndi chifukwa chiyani mukudya ndi kumwa pamodzi ndi amisonkho ndi ochimwa?”

Onani mutuwo Koperani




Luka 5:30
16 Mawu Ofanana  

amene ati, Ima pa wekha, usadze chifupi ndi ine, pakuti ine ndili woyera kupambana iwe; amenewa ndiwo utsi m'mphuno mwanga, moto woyaka tsiku lonse.


Chifukwa kuti ngati muwakonda akukondana ndi inu mphotho yanji muli nayo? Kodi angakhale amisonkho sachita chomwecho?


Ndipo Afarisi, pakuona ichi, ananena kwa ophunzira ake, Chifukwa ninji Mphunzitsi wanu alinkudya pamodzi ndi amisonkho ndi ochimwa?


Ndipo alembi a kwa Afarisi, pakuona kuti alinkudya nao ochimwa ndi amisonkho, ananena ndi ophunzira ake, Uyu akudya ndi kumwa nao amisonkho ndi ochimwa.


Pakuti Afarisi, ndi Ayuda onse sakudya osasamba m'manja ao, kuti asungire mwambo wa akulu;


Ndipo anawafunsa iwo, Mufunsana nao chiyani?


Mfarisiyo anaimirira napemphera izi mwa yekha, Mulungu, ndikuyamikani kuti sindili monga anthu onse ena, opambapamba, osalungama, achigololo, kapenanso monga wamsonkho uyu;


Ndipo m'mene anachiona anadandaula onse, nanena, Analowa amchereze munthu ali wochimwa.


Ndipo panali tsiku limodzi la masiku awo, Iye analikuphunzitsa; ndipo analikukhalapo Afarisi ndi aphunzitsi a malamulo, amene anachokera kumidzi yonse ya ku Galileya, ndi Yudeya ndi Yerusalemu: ndipo mphamvu ya Ambuye inali ndi Iye yakuwachiritsa.


Ndipo alembi ndi Afarisi anayamba kuyesayesa mumtima mwao, kuti, Ndani Uyu alankhula zomchitira Mulungu mwano? Ndani angathe kukhululukira machimo, koma Mulungu yekha?


Mwana wa Munthu wafika wakudya ndi wakumwa; ndipo munena, Onani, munthu wosusuka ndi wakumwaimwa vinyo, bwenzi la amisonkho ndi anthu ochimwa!


Koma Mfarisi, amene adamuitana Iye, pakuona, ananena mwa yekha, nati, Akadakhala mneneri uyu akadazindikira ali yani, ndi wotani mkaziyo womkhudza Iye, chifukwa ali wochimwa.


Ndipo chidauka chipolowe chachikulu, ndipo alembi ena a kwa Afarisi anaimirira, natsutsana, nanena, Sitipeza choipa chilichonse mwa munthuyu; ndipo nanga bwanji ngati mzimu kapena mngelo walankhula naye?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa