Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 4:27 - Buku Lopatulika

27 Ndipo munali akhate ambiri mu Israele masiku a Elisa mneneri; ndipo palibe mmodzi wa iwo anakonzedwa, koma Naamani yekha wa ku Siriya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Ndipo munali akhate ambiri m'Israele masiku a Elisa mneneri; ndipo palibe mmodzi wa iwo anakonzedwa, koma Naamani yekha wa ku Siriya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Panalinso akhate ambiri pakati pa Aisraele nthaŵi ya mneneri Elisa, komabe panalibe ndi mmodzi yemwe mwa iwo aja amene adachiritsidwa. Amene adachiritsidwa ndi Namani yekha wa ku dziko la Siriya.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Ndipo kunali akhate ambiri ku Israeli mʼnthawi ya mneneri Elisa, koma panalibe mmodzi mwa iwo anachiritsidwa kupatula Naamani wa ku Siriya.”

Onani mutuwo Koperani




Luka 4:27
10 Mawu Ofanana  

Ngati pali munthu wakumphunzitsa Mulungu nzeru? Popeza Iye aweruza mlandu iwo okwezeka.


Mutsutsana ndi Iye chifukwa ninji? Popeza pa zake zonse sawulula chifukwa.


Anamuikira njira yake ndani? Adzati ndani, Mwachita chosalungama?


ndi okhala padziko lapansi onse ayesedwa achabe; ndipo Iye achita mwa chifuniro chake m'khamu la kumwamba ndi mwa okhala padziko lapansi; ndipo palibe woletsa dzanja lake, kapena wakunena naye, Muchitanji?


Kuti analowa m'nyumba ya Mulungu, nadya mikate yoonetsa, imene yosaloleka kudya iye kapena amene anali naye, koma ansembe okhaokha.


Ndipo Yesu anatambalitsa dzanja lake, namkhudza iye, nati, Ndifuna; takonzedwa. Ndipo pomwepo khate lake linachoka.


Ndipo onse a m'sunagogemo anadzala ndi mkwiyo pakumva izi;


Pamene ndinakhala nao, Ine ndinalikuwasunga iwo m'dzina lanu amene mwandipatsa Ine; ndipo ndinawasunga, ndipo sanatayike mmodzi yense wa iwo, koma mwana wa chitayiko, kuti lembo likwaniridwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa