Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 4:23 - Buku Lopatulika

23 Ndipo anati kwa iwo, Kwenikweni mudzati kwa Ine nkhani iyi, Sing'anga iwe, tadzichiritsa wekha: zonse zija tazimva zinachitidwa ku Kapernao, muzichitenso zomwezo kwanu kuno.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Ndipo anati kwa iwo, Kwenikweni mudzati kwa Ine nkhani iyi, Sing'anga iwe, tadzichiritsa wekha: zonse zija tazimva zinachitidwa ku Kapernao, muzichitenso zomwezo kwanu kuno.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Apo Yesu adaŵauza kuti, “Ndithudi mudzandiwuza mwambi uja wakuti, ‘Iwe sing'anga, dzichiritse wekha.’ Mudzatinso, ‘Tidamva zimene mudachita ku Kapernao, tsono muchitenso zomwezo kwanu kuno.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, mudzandiwuza mwambi uwu: Singʼanga, dzichiritse wekha! Chitanso mʼmudzi wa kwanu kuno zimene ife tamva kuti Iwe unazichita ku Kaperenawo.”

Onani mutuwo Koperani




Luka 4:23
20 Mawu Ofanana  

Ndipo pofika kudziko la kwao, anaphunzitsa iwo m'sunagoge mwao, kotero kuti anazizwa, nanena, Uyu adazitenga kuti nzeru zimenezi ndi zamphamvu izi?


ndipo anachoka ku Nazarete nadza nakhalitsa Iye mu Kapernao wa pambali pa nyanja, m'malire a Zebuloni ndi Nafutali:


Ndipo Yesu anayendayenda mu Galileya monse, analikuphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu, nachiritsa nthenda zonse ndi kudwala konse mwa anthu.


Ndipo Iye anatuluka kumeneko; nafika kudziko la kwao; ndipo ophunzira ake anamtsata.


Ndipo pamene iwo anatha zonse monga mwa chilamulo cha Ambuye, anabwera ku Galileya, kumzinda kwao, ku Nazarete.


Ndipo anatsika nao pamodzi nadza ku Nazarete; nawamvera iwo: ndipo amake anasunga zinthu izi zonse mumtima mwake.


Ndipo anadza ku Nazarete, kumene analeredwa; ndipo tsiku la Sabata analowa m'sunagoge, monga anazolowera, naimiriramo kuwerenga m'kalata.


Ndipo Iye anatsika nadza ku Kapernao, ndiwo mzinda wa ku Galileya. Ndipo analikuwaphunzitsa iwo pa Sabata; ndipo anadabwa ndi chiphunzitso chake;


Ndipo Yesu anamdzudzula iye, nanena, Tonthola, nutuluke mwa iye. Ndipo chiwandacho m'mene chinamgwetsa iye pakati, chinatuluka mwa iye chosampweteka konse.


Kapena ungathe bwanji kunena kwa mbale wako, Mbale iwe, leka ndichotse kachitsotso kali m'diso lako, wosayang'anira iwe mwini mtanda uli m'diso lako? Wonyenga iwe! Yamba wachotsa mtandawo m'diso lako, ndipo pomwepo udzayang'anitsa bwino kuchotsa kachitsotso ka m'diso la mbale wako.


Pamenepo mkazi anasiya mtsuko wake, namuka mumzinda, nanena ndi anthu,


Kotero kuti ife sitidziwanso munthu tsopano monga mwa thupi; ndipo ngati tazindikira Khristu monga mwa thupi, koma tsopano sitimzindikiranso motero.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa