Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 4:22 - Buku Lopatulika

22 Ndipo onse anamchitira Iye umboni nazizwa ndi mau a chisomo akutuluka m'kamwa mwake; nanena, Kodi uyu si mwana wa Yosefe?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Ndipo onse anamchitira Iye umboni nazizwa ndi mau a chisomo akutuluka m'kamwa mwake; nanena, Kodi uyu si mwana wa Yosefe?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Anthu onse adamtamanda, nkumadabwa ndi mau ogwira mtima amene Iye ankalankhula. Anthuwo ankati, “Kodi uyu si mwana uja wa Yosefeyu?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Onse anayankhula zabwino za Iye ndipo anadabwa ndi mawu ogwira moyo amene anatuluka mʼkamwa mwake. Iwo anafunsa kuti, “Kodi uyu si mwana wa Yosefe?”

Onani mutuwo Koperani




Luka 4:22
20 Mawu Ofanana  

Inu ndinu wokongola ndithu koposa ana a anthu; anakutsanulirani chisomo pa milomo yanu, chifukwa chake Mulungu anakudalitsani kosatha.


Ndipo pindulani, mu ukulu wanu yendani, kaamba ka choonadi ndi chifatso ndi chilungamo; ndipo dzanja lanu lidzakuphunzitsani zoopsa.


Milomo ya wolungama idziwa zokondweretsa; koma m'kamwa mwa oipa munena zokhota.


Wanzeru mtima adzatchedwa wochenjera; ndipo kukoma kwa milomo kuonjezera kuphunzira.


Mau oyenera a pa nthawi yake akunga zipatso zagolide m'nsengwa zasiliva.


Mau a m'kamwa mwa munthu wanzeru nga chisomo; koma milomo ya chitsiru idzachimeza.


M'kamwa mwake muli mokoma; inde, ndiye wokondweretsa ndithu. Ameneyu ndi wokondedwa wanga, ameneyu ndi bwenzi langa, ana aakazi inu a ku Yerusalemu.


Ambuye Yehova wandipatsa Ine lilime la ophunzira, kuti ndidziwe kunena mau akuchirikiza iye amene ali wolema. Iye andigalamutsa m'mawa ndi m'mawa, nagalamutsa khutu langa kuti limve monga ophunzira.


Ndipo onse amene anamva Iye anadabwa ndi chidziwitso chake, ndi mayankho ake.


Ndipo m'mene anamuona Iye, anadabwa; ndipo amake anati kwa Iye, Mwanawe, wachitiranji ife chotero; taona, atate wako ndi ine tinalikufunafuna Iwe ndi kuda nkhawa.


Pakuti Ine ndidzakupatsani inu kamwa ndi nzeru, zimene adani anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.


Ndipo anayamba kunena kwa iwo, kuti, Lero lembo ili lakwanitsidwa m'makutu anu.


Filipo anapeza Natanaele, nanena naye, Iye amene Mose analembera za Iye m'chilamulo, ndi aneneri, tampeza, ndiye Yesu mwana wa Yosefe wa ku Nazarete.


Ndipo iwo ananena, Si Yesu uyu, mwana wa Yosefe, atate wake ndi amai wake tiwadziwa? Anena bwanji tsopano, kuti, Ndinatsika Kumwamba?


Anyamatawo anayankha, Nthawi yonse palibe munthu analankhula chotero.


Ndipo sanathe kuipambana nzeru ndi Mzimu amene analankhula naye.


mau olama osatsutsika; kuti iye wakutsutsana achite manyazi, posakhala nako kanthu koipa kakutinenera ife.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa