Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 24:21 - Buku Lopatulika

21 Ndipo tinayembekeza ife kuti Iye ndiye wakudzayo kudzaombola Israele. Komatunso, pamodzi ndi izi zonse lero ndilo tsiku lachitatu kuyambira zidachitika izi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Ndipo tinayembekeza ife kuti Iye ndiye wakudzayo kudzaombola Israele. Komatunso, pamodzi ndi izi zonse lero ndilo tsiku lachitatu kuyambira zidachitika izi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Ife tinkayembekeza kuti Iyeyo ndiye adzaombole Aisraele, koma ha! Ndi dzana pamene zidachitika zonsezi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 koma ife tinkayembekezera kuti Iye ndiye amene akanawombola Israeli. Ndipo kuwonjeza apo, lero ndi tsiku lachitatu chichitikireni izi.

Onani mutuwo Koperani




Luka 24:21
8 Mawu Ofanana  

Ndipo adzaombola Israele ku mphulupulu zake zonse.


Ndipo Mombolo adzafika ku Ziyoni, ndi kwa iwo amene atembenuka kusiya kulakwa mwa Yakobo, ati Yehova.


Wolemekezeka Ambuye, Mulungu wa Israele; chifukwa Iye anayang'ana, nachitira anthu ake chiombolo.


Ndipo iye anafikako pa nthawi yomweyo, navomerezanso kutama Mulungu, nalankhula za Iye kwa anthu onse akuyembekeza chiombolo cha Yerusalemu.


Pamenepo iwowa, atasonkhana pamodzi, anamfunsa Iye, nanena, Ambuye, kodi nthawi ino mubwezera ufumu kwa Israele?


Kodi ufuna kundipha ine, monga muja unapha Mwejipito dzulo?


Ndipo aimba nyimbo yatsopano, ndi kunena, Muyenera kulandira bukulo, ndi kumasula zizindikiro zake; chifukwa mwaphedwa, ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa