Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 23:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo Herode, pamene anaona Yesu, anakondwa ndithu; pakuti anayamba kale kufuna kumpenya Iye, chifukwa anamva za Iye; nayembekeza kuona chizindikiro china chochitidwa ndi Iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo Herode, pamene anaona Yesu, anakondwa ndithu; pakuti anayamba kale kufuna kumpenya Iye, chifukwa anamva za Iye; nayembekeza kuona chizindikiro china chochitidwa ndi Iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Herode poona Yesu, adakondwa kwambiri, chifukwa ankamva za Iye, mwakuti kwa nthaŵi yaitali ankafuna atamuwona. Ankayembekeza kuti aone Yesu akuchita chozizwitsa china.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Herode ataona Yesu, anakondwa kwambiri, chifukwa kwa nthawi yayitali, ankafunitsitsa atamuona. Kuchokera pa zimene anamva za Iye, anayembekezera kuti achita zodabwitsa.

Onani mutuwo Koperani




Luka 23:8
8 Mawu Ofanana  

Koma Naamani adapsa mtima, nachoka, nati, Taona, ndinati m'mtima mwanga, kutuluka adzanditulukira, nadzaima ndi kuitana pa dzina la Yehova Mulungu wake, ndi kuweyula dzanja lake pamalopo, ndi kuchiritsa wakhateyo.


Nthawi imeneyo Herode mfumu anamva mbiri ya Yesu,


Ndipo mfumu Herode anamva izi; pakuti dzina lake lidamveka; ndipo ananena, kuti, Yohane Mbatizi wauka kwa akufa, ndipo chifukwa chake mphamvu izi zichitachita mwa Iye.


Ndipo anadziitanira khamulo la anthu pamodzi ndi ophunzira ake, nati kwa iwo, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikanize yekha, nanyamule mtanda wake, nanditsate Ine.


Ndipo anati kwa iwo, Kwenikweni mudzati kwa Ine nkhani iyi, Sing'anga iwe, tadzichiritsa wekha: zonse zija tazimva zinachitidwa ku Kapernao, muzichitenso zomwezo kwanu kuno.


nanena, Ndipatseni inenso ulamuliro umene, kuti aliyense amene ndikaika manja pa iye, alandire Mzimu Woyera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa