Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 23:44 - Buku Lopatulika

44 Ndipo ora lake pamenepo linali ngati lachisanu ndi chimodzi. Ndipo panali mdima padziko lonse kufikira ora lachisanu ndi chinai, ndipo dzuwa linada.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

44 Ndipo ora lake pamenepo linali ngati lachisanu ndi chimodzi. Ndipo panali mdima pa dziko lonse kufikira ora lachisanu ndi chinai, ndipo dzuwa linada.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

44 Nthaŵi itakwana ngati 12 koloko masana, padaagwa mdima pa dziko lonse mpaka pa 3 koloko,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

44 Linali tsopano pafupi ora lachisanu ndi chimodzi, ndipo mdima unagwa pa dziko lonse mpaka ora lachisanu ndi chinayi,

Onani mutuwo Koperani




Luka 23:44
12 Mawu Ofanana  

Anatumiza mdima ndipo kunada; ndipo sanapikisane nao mau ake.


Dzuwa lidzasanduka mdima, ndi mwezi udzasanduka mwazi, lisanadze tsiku la Yehova lalikulu ndi loopsa.


Tsoka inu akufuna tsiku la Yehova? Mudzapindulanji nalo tsiku la Yehova? Ndilo mdima, si kuunika ai.


Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo, ati Ambuye Yehova, ndidzalowetsa dzuwa usana, ndi kudetsa dziko pausana poyera.


Ndipo ora lachisanu ndi chimodzi panali mdima padziko lonse, kufikira ora lachisanu ndi chinai.


ndi manda anatseguka, ndi mitembo yambiri ya anthu oyera mtima, akugona kale, inauka;


Ndipo pamene kenturiyo, woimirirapo popenyana ndi Iye, anaona kuti anapereka mzimu kotero, anati, Zoonadi, munthu uyu anali Mwana wa Mulungu.


Koma linali tsiku lokonza Paska; panali monga ora lachisanu ndi chimodzi. Ndipo ananena kwa Ayuda, Taonani, mfumu yanu!


dzuwa lidzasanduka mdima, ndi mwezi udzasanduka mwazi, lisanadze tsiku la Ambuye, lalikulu ndi loonekera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa