Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 22:41 - Buku Lopatulika

41 Ndipo anapatukana nao kutalika kwake ngati kuponya mwala, nagwada pansi napemphera,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

41 Ndipo anapatukana nao kutalika kwake ngati kuponya mwala, nagwada pansi napemphera,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

41 Tsono adapatukana nawo kadera, kutalika kwake ngati pamene mwala ungafike munthu atauponya. Apo adagwada pansi nayamba kupemphera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

41 Iye anapita patsogolo pangʼono patali ngati kuponya mwala, anagwada napephera kuti,

Onani mutuwo Koperani




Luka 22:41
9 Mawu Ofanana  

Ndipo anamuka patsogolo pang'ono, nagwa nkhope yake pansi, napemphera, nati, Atate ngati nkutheka, chikho ichi chindipitirire Ine; koma si monga ndifuna Ine, koma Inu.


Ndipo Iye anapita m'tsogolo pang'ono, nagwa pansi, napemphera kuti ngati nkutheka nthawi imene impitirire.


Mfarisiyo anaimirira napemphera izi mwa yekha, Mulungu, ndikuyamikani kuti sindili monga anthu onse ena, opambapamba, osalungama, achigololo, kapenanso monga wamsonkho uyu;


Koma wamsonkhoyo alikuima patali sanafune kungakhale kukweza maso kumwamba, komatu anadziguguda pachifuwa pake nanena, Mulungu, mundichitire chifundo, ine wochimwa.


Ndipo m'mene ananena izi, anagwada pansi, napemphera ndi iwo onse.


Ndipo kunali pamene tidatsiriza masikuwa, tidachoka ndi kunka ulendo wathu; ndipo iwo onse, akazi ndi ana, anatiperekeza kufikira kutuluka m'mzinda; ndipo pogwadira pa mchenga wa kunyanja, tinapemphera,


Ndipo m'mene anagwada pansi, anafuula ndi mau aakulu, Ambuye, musawaikire iwo tchimo ili. Ndipo m'mene adanena ichi, anagona tulo.


Koma Petro anawatulutsa onse, nagwada pansi, napemphera; ndipo potembenukira kumtembo anati, Tabita, uka. Ndipo anatsegula maso ake; ndipo pakuona Petro, anakhala tsonga.


Ameneyo, m'masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa