Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 22:22 - Buku Lopatulika

22 Pakuti Mwana wa Munthu amukatu, monga kunaikidwiratu; koma tsoka munthuyo amene ampereka!

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Pakuti Mwana wa Munthu amukatu, monga kunaikidwiratu; koma tsoka munthuyo amene ampereka!

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Mwana wa Munthu akukaphedwadi, monga momwe Mulungu adazikonzeratu kale. Komabe ali ndi tsoka munthu amene akukapereka Mwana wa Munthuyo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Mwana wa Munthu apita monga mmene zinalembedwera, koma tsoka kwa munthu amene amupereka Iye.”

Onani mutuwo Koperani




Luka 22:22
26 Mawu Ofanana  

ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitendeni chake.


Galamuka, lupanga, pa mbusa wanga, ndi pa munthu mnzanga wa pamtima, ati Yehova wa makamu; kantha mbusa, ndi nkhosa zidzabalalika; koma ndidzabwezera dzanja langa pa zazing'onozo.


Mwana wa Munthu achokatu, monga kunalembedwa za Iye; koma tsoka ali nalo munthu amene Mwana wa Munthu aperekedwa ndi iye! Kukadakhala bwino kwa munthuyo ngati sakadabadwa.


Ndipo iye anataya pansi ndalamazo pa Kachisi, nachokapo, nadzipachika yekha pakhosi.


Pakuti Mwana wa Munthu amukadi, monga kwalembedwa za Iye; koma tsoka munthuyo amene apereka Mwana wa Munthu! Kukadakhala bwino kwa munthu ameneyo ngati sakadabadwa iye.


Ndipo anayamba kufunsana mwa iwo okha, ndiye yani mwa iwo amene adzachita ichi.


ndipo anati kwa iwo, Kotero kwalembedwa, kuti Khristu amve zowawa, nauke kwa akufa tsiku lachitatu;


Pamene ndinakhala nao, Ine ndinalikuwasunga iwo m'dzina lanu amene mwandipatsa Ine; ndipo ndinawasunga, ndipo sanatayike mmodzi yense wa iwo, koma mwana wa chitayiko, kuti lembo likwaniridwe.


Ndipo anatilamulira ife tilalikire kwa anthu, ndipo tichite umboni kuti Uyu ndiye amene aikidwa ndi Mulungu akhale woweruza amoyo ndi akufa.


chifukwa anapangira tsiku limene adzaweruza dziko lokhalamo anthu m'chilungamo, ndi munthu amene anamuikiratu; napatsa anthu onse chitsimikizo, pamene anamuukitsa Iye kwa akufa.


ameneyo, woperekedwa ndi uphungu woikidwa ndi kudziwiratu kwa Mulungu, inu mwampachika ndi kumupha ndi manja a anthu osaweruzika;


ndi kusanthula nthawi yiti, kapena nthawi yanji Mzimu wa Khristu wokhala mwa iwo analozera, pakuchitiratu umboni wa masautso a Khristu, ndi ulemerero wotsatana nao.


Ndipo m'chisiriro adzakuyesani malonda ndi mau onyenga; amene chiweruzo chao sichinachedwe ndi kale lomwe, ndipo chitayiko chao sichiodzera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa