Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 21:6 - Buku Lopatulika

6 Zinthu izi muziona, adzafika masiku, pamenepo sudzasiyidwa pano mwala pamwala unzake, umene sudzagwetsedwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Zinthu izi muziona, adzafika masiku, pamenepo sudzasiyidwa pano mwala pa mwala unzake, umene sudzagwetsedwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 “Kunena za zinthu mukuziwonazi, masiku adzabwera mwakuti sipadzatsala konse mwala ndi umodzi womwe pamwamba pa mwala unzake: yonse adzaigumula.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 “Koma zimene mukuziona panozi, nthawi idzafika pamene ngakhale mwala umodzi omwe sudzakhala pa unzake; uliwonse udzagwetsedwa pansi.”

Onani mutuwo Koperani




Luka 21:6
20 Mawu Ofanana  

Mika Mmoreseti ananenera masiku a Hezekiya mfumu ya Yuda; ndipo iye ananena kwa anthu onse a Yuda, kuti, Yehova wa makamu atero: Ziyoni adzalimidwa ngati munda, Yerusalemu adzakhala miunda, ndi phiri la nyumba longa misanje ya nkhalango.


pamenepo ndidzayesa nyumba iyi ifanane ndi Silo, ndipo ndidzayesa mzinda uwu chitemberero cha kwa mitundu yonse ya dziko lapansi.


Bwanji mwanenera m'dzina la Yehova, kuti, Nyumba iyi idzafanana ndi Silo, mzinda uwu udzakhala bwinja lopanda wokhalamo? Ndipo anthu onse anamsonkhanira Yeremiya m'nyumba ya Yehova.


Ha! Golide wagugadi; golide woona woposa wasandulika; miyala ya malo opatulika yakhuthulidwa pa malekezero a makwalala onse.


paphiri la Ziyoni lopasukalo ankhandwe ayendapo.


Momwemo Ziyoni adzalimidwa ngati munda chifukwa cha inu, ndi mu Yerusalemu mudzasanduka miunda, ndi phiri la nyumba ngati misanje ya m'nkhalango.


Tsegula pa makomo ako Lebanoni, kuti moto uthe mikungudza yako.


Pakuti ndidzasonkhanitsa amitundu onse alimbane ndi Yerusalemu; ndipo mzindawo udzalandidwa, ndi nyumba zidzafunkhidwa, ndi akazi adzakakamizidwa; ndi limodzi la magawo awiri la mzinda lidzatuluka kunka kundende, koma anthu otsala sadzaonongeka m'mzindamo.


Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Simuona izi zonse kodi? Indetu ndinena kwa inu, Sipadzakhala pano mwala umodzi pa unzake, umene sudzagwetsedwa.


Ndipo Yesu anati kwa iye, Kodi waona nyumba izi zazikulu? Sudzasiyidwa pano mwala umodzi pamwamba pa unzake, umene sudzagwetsedwa.


Ndipo iwo anamfunsa Iye, nati, Mphunzitsi, nanga zinthu izi zidzaoneka liti? Ndipo chizindikiro ndi chiyani pamene izi ziti zichitike?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa