Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 21:21 - Buku Lopatulika

21 Pamenepo iwo ali mu Yudeya athawire kumapiri, ndi iwo ali m'kati mwa uwo atuluke, ndi iwo ali kuminda asalowemo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Pamenepo iwo ali m'Yudeya athawire kumapiri, ndi iwo ali m'kati mwa uwo atuluke, ndi iwo ali kumilaga asalowemo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Pamenepo amene ali m'Yudeya athaŵire ku mapiri, amene ali mumzinda atulukemo, ndipo amene ali ku minda asadzaloŵenso mumzindamo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Pamenepo amene ali ku Yudeya adzathawire ku mapiri, amene ali mu mzinda adzatulukemo, ndi amene ali ku midzi asadzalowe mu mzinda.

Onani mutuwo Koperani




Luka 21:21
13 Mawu Ofanana  

Ndipo panali pamene anawatulutsa iwo kunja, anati, Tapulumuka ndi moyo wako; usacheuke, usakhale pachigwa paliponse; thawira kuphiri, kuti unganyeke.


Koma mkazi wake anacheuka ali pambuyo pake pa Loti, nasanduka mwala wamchere.


Wochenjera aona zoipa, nabisala; koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.


Koma panali, pamene Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anadza m'dzikomu, ife tinati, Tiyeni tinke ku Yerusalemu chifukwa tiopa nkhondo ya Ababiloni, ndi nkhondo ya Aramu; ndipo tikhala mu Yerusalemu.


pamenepo Yeremiya anatuluka mu Yerusalemu kumuka kudziko la Benjamini, kukalandira gawo lake kumeneko.


Ananu a Benjamini, pulumukani pothawa pakati pa Yerusalemu, ombani lipenga mu Tekowa, kwezani chizindikiro mu Betehakeremu; pakuti chaoneka choipa chotuluka m'mpoto ndi kuononga kwakukulu.


Ndipo ananena ndi khamulo, nati, Chokanitu ku mahema a anthu awa oipa, musamakhudza kanthu kao kalikonse, mungaonongeke m'zochimwa zao zonse.


Ndipo pa kubadwa kwake kwa Yesu mu Betelehemu wa Yudeya m'masiku a Herode mfumu, onani, Anzeru a kum'mawa anafika ku Yerusalemu,


pomwepo iwo ali mu Yudeya athawire kumapiri:


ndi iye amene ali pamwamba pa tsindwi asatsike, kapena asalowe kukatulutsa kanthu m'nyumba mwake;


Ndipo ndinamva mau ena ochokera Kumwamba, nanena, Tulukani m'menemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa