Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 21:16 - Buku Lopatulika

16 Koma mudzaperekedwa ngakhale ndi akukubalani, ndi abale, ndi a fuko lanu, ndi abwenzi anu; ndipo ena a inu adzakuphani.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Koma mudzaperekedwa ngakhale ndi akukubalani, ndi abale, ndi a fuko lanu, ndi abwenzi anu; ndipo ena a inu adzakuphani.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Makolo anu omwe, abale anu, anansi anu, ndi abwenzi anu, amenewo adzakuperekani kwa adani anu, ndipo ena mwa inu mudzaphedwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Inu mudzaperekedwa ndi makolo anu, abale, anansi ndi abwenzi anu ndipo ena mwa inu adzakuphani.

Onani mutuwo Koperani




Luka 21:16
14 Mawu Ofanana  

Pakuti ngakhale abale ako, ndi nyumba ya atate wako, ngakhale iwo anakunyenga iwe; ngakhale anakufuulira iwe; usamvere iwo, ngakhale anena nawe mau abwino.


Muchenjere naye yense mnansi wake, musakhulupirire yense mbale wake; pakuti abale onse amanyenga, ndipo anansi onse adzayenda ndi maugogodi.


Ndipo mbale adzapereka mbale wake kuimfa, ndi atate mwana wake: ndipo ana adzatsutsa akuwabala, nadzawafetsa iwo.


Ndipo mbale adzapereka mbale wake kuti amuphe, ndi atate mwana wake; ndi ana adzayambana ndi akuwabala, nadzawaphetsa.


Adzatsutsana atate ndi mwana wake, ndi mwana ndi atate wake; amake adzatsutsana ndi mwana wamkazi, ndi mwana wamkazi ndi amake, mpongozi adzatsutsana ndi mkazi wa mwana wake, ndi mkaziyo ndi mpongozi wake.


Pakuti Ine ndidzakupatsani inu kamwa ndi nzeru, zimene adani anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.


Ndipo anthu onse adzadana ndi inu chifukwa cha dzina langa.


Ndipo adapha ndi lupanga Yakobo mbale wa Yohane.


Ndipo anamponya miyala Stefano, alikuitana Ambuye, ndi kunena, Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga.


Ndipo iwo anampambana iye chifukwa cha mwazi wa Mwanawankhosa, ndi chifukwa cha mau a umboni wao; ndipo sanakonde moyo wao kungakhale kufikira imfa.


Ndidziwa kumene ukhalako kuja kuli mpando wachifumu wa Satana; ndipo ugwira dzina langa, osakaniza chikhulupiriro changa, angakhale m'masiku a Antipa, mboni yanga, wokhulupirika wanga, amene anaphedwa pali inu, kuja akhalako Satana.


Ndipo pamene adamasula chizindikiro chachisanu, ndinaona pansi pa guwa la nsembe mizimu ya iwo adaphedwa chifukwa cha mau a Mulungu, ndi chifukwa cha umboni umene anali nao:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa