Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 21:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo Yesu anakweza maso, naona anthu eni chuma alikuika zopereka zao mosungiramo ndalama.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo Yesu anakweza maso, naona anthu eni chuma alikuika zopereka zao mosungiramo ndalama.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Yesu atakweza maso, adaona anthu olemera akuponya zopereka zao m'bokosi la ndalama m'Nyumba ya Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Yesu atayangʼana, anaona olemera akuyika mphatso zawo mu chosungira ndalama za mʼNyumba ya Mulungu.

Onani mutuwo Koperani




Luka 21:1
12 Mawu Ofanana  

nachotsa chuma cha m'nyumba ya Yehova, ndi chuma cha m'nyumba ya mfumu; inde anachotsa chonsecho, nachotsanso zikopa zagolide zonse adazipanga Solomoni.


Ndipo Yehoyada wansembe anatenga bokosi, naboola chiboo pa chivundikiro chake, naliika pafupi paguwa la nsembe, ku dzanja lamanja polowera nyumba ya Yehova; ndipo ansembe akusunga pakhomo anaikamo ndalama zonse anabwera nazo anthu kunyumba ya Yehova.


Natulutsa kuchotsa komweko chuma chonse cha nyumba ya Yehova, ndi chuma cha nyumba ya mfumu, naduladula zipangizo zonse zagolide adazipanga Solomoni mfumu ya Israele mu Kachisi wa Yehova, monga Yehova adanena.


Ndi zipangizo zonse za nyumba ya Mulungu, zazikulu ndi zazing'ono, ndi chuma cha nyumba ya Yehova, ndi chuma cha mfumu, ndi cha akalonga ake, anabwera nazo zonsezi ku Babiloni.


Ndinaikanso osunga chuma, asunge nyumba za chuma: Selemiya wansembe, ndi Zadoki mlembi; ndi wa Alevi, Pedaya; ndi wakuwathandiza, Hanani mwana wa Zakuri, mwana wa Mataniya; popeza anayesedwa okhulupirika ndi udindo wao, ndiwo kugawira abale ao.


Ndipo ansembe aakulu anatenga ndalamazo, nati, Sikuloledwa kuziika m'chosonkhera ndalama za Mulungu, chifukwa ndizo mtengo wa mwazi.


amene aononga nyumba za akazi amasiye, ndipo monyenga achita mapemphero aatali; amenewo adzalandira kulanga koposa.


Mau awa analankhula m'nyumba yosungiramo chuma cha Mulungu pophunzitsa mu Kachisi; ndipo palibe munthu anamgwira Iye, pakuti nthawi yake siinafike.


Koma siliva yense, ndi golide yense, ndi zotengera za mkuwa ndi chitsulo zikhala chopatulikira Yehova; zilowe m'mosungira chuma cha Yehova.


Ndipo anatentha mzinda ndi moto, ndi zonse zinali m'mwemo; koma siliva ndi golide ndi zotengera zamkuwa ndi zachitsulo anaziika m'mosungira chuma cha nyumba ya Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa