Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 2:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo Yosefe yemwe anakwera kuchokera ku Galileya, kumzinda wa Nazarete, kunka ku Yudeya, kumzinda wa Davide, dzina lake Betelehemu, chifukwa iye anali wa banja ndi fuko lake la Davide;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo Yosefe yemwe anakwera kuchokera ku Galileya, kumudzi wa Nazarete, kunka ku Yudeya, kumudzi wa Davide, dzina lake Betelehemu, chifukwa iye anali wa banja ndi fuko lake la Davide;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Yosefe nayenso adanyamuka kuchokera ku Nazarete, mudzi wa ku Galileya. Adapita ku Yudeya, ku mudzi wa mfumu Davide, dzina lake Betelehemu, chifukwa anali wa m'banja ndi fuko la Davideyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Choncho Yosefe anachoka ku Nazareti ku Galileya kupita ku Yudeya, ku Betelehemu ku mudzi wa Davide, chifukwa anali wa banja ndi fuko la Davide.

Onani mutuwo Koperani




Luka 2:4
24 Mawu Ofanana  

Ndipo anafa Rakele, naikidwa panjira ya ku Efurata (ndiwo Betelehemu).


Tsono ine, pamene ndinachokera ku Padani, Rakele anamwalira pambali panga m'dziko la Kanani m'njira, itatsala nthawi yaing'ono tisadafike ku Efurata; ndipo ndidamuika iye pamenepo panjira ya ku Efurata (ndiwo Betelehemu).


Koma iwe, Betelehemu Efurata, ndiwe wamng'ono kuti ukhale mwa zikwi za Yuda, mwa iwe mudzanditulukira wina wakudzakhala woweruza mu Israele; matulukiro ake ndiwo a kale lomwe, kuyambira nthawi yosayamba.


Koma pakusinkhasinkha iye zinthu izi, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iye m'kulota, nanena, Yosefe, mwana wa Davide, usaope kudzitengera wekha Maria mkazi wako; pakuti icho cholandiridwa mwa iye chili cha Mzimu Woyera.


nadza nakhazikika m'mzinda dzina lake Nazarete kuti chikachitidwe chonenedwa ndi aneneri kuti, Adzatchedwa Mnazarayo.


Ndipo onse anamuka kulembedwa, munthu aliyense kumzinda wake.


kukalembedwa iye mwini pamodzi ndi Maria, wopalidwa naye ubwenzi; ndi uyu anali ndi pakati.


Ndipo anadza ku Nazarete, kumene analeredwa; ndipo tsiku la Sabata analowa m'sunagoge, monga anazolowera, naimiriramo kuwerenga m'kalata.


Natanaele anati kwa iye, Ku Nazarete nkutha kuchokera kanthu kabwino kodi? Filipo ananena naye, Tiye ukaone.


Kodi sichinati chilembo kuti Khristu adza kutuluka mwa mbeu ya Davide, ndi kuchokera ku Betelehemu, kumudzi kumene kunali Davide?


Namuka iwo awiriwo mpaka anafika ku Betelehemu. Ndipo kunali pakufika iwo ku Betelehemu, mudzi wonse unapokosera za iwo; nati, Kodi uyu ndi Naomi?


Ndipo taona, Bowazi anafuma ku Betelehemu, nati kwa ocheka, Yehova akhale nanu. Namyankha iwo, Yehova akudalitseni.


Pamenepo anthu onse anali kuchipata, ndi akulu, anati, Tili mboni ife. Yehova achite kuti mkazi wakulowayo m'nyumba mwako ange Rakele ndi Leya, amene anamanga nyumba ya Israele, iwo awiri; nuchite iwe moyenera mu Efurata, numveke mu Betelehemu;


Ndi akazi anansi ake anamutcha dzina, ndi kuti, Kwa Naomi kwambadwira mwana; namutcha dzina lake Obedi; ndiye atate wa Yese atate wa Davide.


Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Iwe ukuti ulire chifukwa cha Saulo nthawi yotani, popeza Ine ndinamkana kuti asakhale mfumu ya Israele? Dzaza nyanga yako ndi mafuta, numuke, ndidzakutumiza kwa Yese wa ku Betelehemu; pakuti ndinadzionera mfumu pakati pa ana ake.


Ndipo Samuele anachita chimene Yehova ananena, nadza ku Betelehemu. Ndipo akulu a mzindawo anadza kukomana naye monthunthumira, nati, Mubwera ndi mtendere kodi?


Tsono Davide anali mwana wa Mwefurati uja wa ku Betelehemu ku Yuda, dzina lake ndiye Yese; ameneyu anali nao ana aamuna asanu ndi atatu; ndipo m'masiku a Saulo munthuyo anali nkhalamba, mwa anthu.


Ndipo Saulo anati kwa iye, Mnyamata iwe, ndiwe mwana wa yani? Davide nayankha, Ndili mwana wa kapolo wanu Yese wa ku Betelehemu.


Atate wako akandifuna pang'ono ponse, unene kuti, Davide anandiumirira ndimlole athamangire kwao ku Betelehemu, pakuti kumeneko kuli nsembe ya pachaka ya banja lao lonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa