Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 2:15 - Buku Lopatulika

15 Ndipo panali, pamene angelo anachokera kwa iwo kunka Kumwamba, abusa anati wina ndi mnzake, Tipitiretu ku Betelehemu, tikaone chinthu ichi chidachitika, chimene Ambuye anatidziwitsira ife.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Ndipo panali, pamene angelo anachokera kwa iwo kunka Kumwamba, abusa anati wina ndi mnzake, Tipitiretu ku Betelehemu, tikaone chinthu ichi chidachitika, chimene Ambuye anatidziwitsira ife.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Angelowo atachoka kubwerera Kumwamba, abusa aja adayamba kuuzana kuti, “Tiyeni tipite ku Betelehemu, tikaone zachitikazi, zimene Ambuye atidziŵitsa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Angelowo atabwerera kumwamba, abusawo anati kwa wina ndi mnzake, “Tiyeni ku Betelehemu tikaone zinthu zomwe zachitika, zimene Ambuye atiwuza ife.”

Onani mutuwo Koperani




Luka 2:15
12 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali, pamene Yehova adati akweze Eliya kumwamba ndi kamvulumvulu, Eliya anachokera ku Giligala pamodzi ndi Elisa.


Ndipo kunachitika, akali chiyendere ndi kukambirana, taonani, anaoneka galeta wamoto ndi akavalo amoto, nawalekanitsa awiriwa; Eliya nakwera kumwamba ndi kamvulumvulu.


Ntchito za Yehova nzazikulu, zofunika ndi onse akukondwera nazo.


Ndipo Mose anati, Ndipatuketu, ndikaone chooneka chachikulucho, chitsambacho sichinyeka bwanji.


Mfumu yaikazi ya kumwera adzauka pamlandu pamodzi ndi obadwa amakono, nadzawatsutsa; chifukwa iye anachokera kumathero a dziko lapansi kudzamva nzeru ya Solomoni; ndipo onani, wakuposa Solomoni ali pano.


Ulemerero ukhale kwa Mulungu Kumwambamwamba, ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nao.


Ndipo iwo anadza ndi changu, napeza Maria, ndi Yosefe, ndi mwana wakhanda atagona modyera.


Ndipo kunali, pakuwadalitsa Iye analekana nao, natengedwa kunka Kumwamba.


amene akhala padzanja lamanja la Mulungu, atalowa mu Mwamba; pali angelo, ndi maulamuliro, ndi zimphamvu, zonse zimgonjera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa