Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 19:47 - Buku Lopatulika

47 Ndipo analikuphunzitsa mu Kachisi tsiku ndi tsiku. Koma ansembe aakulu, ndi alembi ndi akulu a anthu anafunafuna kumuononga Iye;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

47 Ndipo analikuphunzitsa m'Kachisi tsiku ndi tsiku. Koma ansembe aakulu, ndi alembi ndi akulu a anthu anafunafuna kumuononga Iye;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

47 Yesu ankaphunzitsa m'Nyumba ya Mulungu tsiku ndi tsiku. Akulu a ansembe, aphunzitsi a Malamulo ndiponso akulu a Ayuda ankafuna kumupha,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

47 Tsiku lililonse amaphunzitsa mʼNyumba ya Mulungu. Koma akulu a ansembe, aphunzitsi amalamulo ndi atsogoleri pakati pa anthu amayesetsa kuti amuphe.

Onani mutuwo Koperani




Luka 19:47
17 Mawu Ofanana  

Ndipo m'mene Iye analowa mu Kachisi, ansembe aakulu ndi akulu a anthu anadza kwa Iye analikuphunzitsa, nanena, Muchita izi ndi ulamuliro wotani? Ndipo ndani anakupatsani ulamuliro wotere?


Nthawi yomweyo Yesu anati kwa makamuwo a anthu, Kodi munatulukira kundigwira Ine ndi malupanga ndi mikunkhu, ngati wachifwamba? Tsiku ndi tsiku ndimakhala mu Kachisi kuphunzitsa, ndipo simunandigwire.


Ndipo ansembe aakulu ndi alembi anamva, nafunafuna momuonongera Iye; pakuti anamuopa, chifukwa khamu lonse la anthu linazizwa ndi chiphunzitso chake.


Ndipo anayesa kumgwira Iye; koma anaopa khamu la anthu, pakuti anazindikira kuti Iye anakamba fanizo ili kuwatsutsa iwo; ndipo anamsiya Iye, nachoka.


Ndipo popita masiku awiri kuli phwando la Paska ndi Mkate wopanda chotupitsa; ndipo ansembe aakulu ndi alembi anafunafuna momchitira chiwembu, ndi kumupha:


Masiku onse ndinali nanu mu Kachisi ndilikuphunzitsa, ndipo simunandigwire Ine; koma ichi chachitika kuti malembo akwaniritsidwe.


ndipo sanapeze chimene akachita; pakuti anthu onse anamlendewera Iye kuti amve.


Ndipo alembi ndi ansembe aakulu anafunafuna kumgwira ndi manja nthawi yomweyo; ndipo anaopa anthu; pakuti anazindikira kuti ananenera pa iwo fanizo ili.


Anafunanso kumgwira Iye; ndipo anapulumuka m'dzanja lao.


Yesu anayankha iye, Ine ndalankhula zomveka kwa dziko lapansi; ndinaphunzitsa Ine nthawi zonse m'sunagoge ndi mu Kachisi, kumene amasonkhana Ayuda onse; ndipo mobisika sindinalankhule kanthu.


Si Mose kodi anakupatsani inu chilamulo, ndipo kulibe mmodzi mwa inu achita chilamulo? Mufuna kundipha chifukwa ninji?


Koma ena mwa iwo anafuna kumgwira Iye; koma palibe munthu anamgwira kumanja.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa