Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 18:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo anatinso kwa ena amene anadzikhulupirira mwa iwo okha kuti ali olungama, napeputsa onse ena, fanizo ili,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo anatinso kwa ena amene anadzikhulupirira mwa iwo okha kuti ali olungama, napeputsa onse ena, fanizo ili,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Yesu adaŵapheranso fanizo anthu ena amene ankadziyesa olungama nkumanyoza anzao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Yesu ananena fanizoli kwa amene amadzikhulupirira mwa iwo okha kuti anali wolungama nanyoza ena onse.

Onani mutuwo Koperani




Luka 18:9
22 Mawu Ofanana  

Pali mbadwo wodziyesa oyera, koma osasamba litsiro lao.


amene ati, Ima pa wekha, usadze chifupi ndi ine, pakuti ine ndili woyera kupambana iwe; amenewa ndiwo utsi m'mphuno mwanga, moto woyaka tsiku lonse.


Imvani mau a Yehova, inu amene munthunthumira ndi mau ake; abale anu amene akudani inu, amene anaponya inu kunja chifukwa cha dzina langa, iwo anati, Yehova alemekezedwe, kuti ife tione kusangalala kwanu; koma iwo adzakhala ndi manyazi.


ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri wansembe aone nthendayi; ndipo taonani, ngati mfundu njosakula, ndipo mulibe tsitsi loyezuka, ndipo mfundu ikaoneka yosakumba kubzola khungu,


Koma iye, pofuna kudziyesa yekha wolungama, anati kwa Yesu, Ndipo mnansi wanga ndani?


Ndipo Afarisi ndi alembi anadandaula nati, Uyu alandira anthu ochimwa, nadya nao.


Ndipo anati kwa iwo, Inu ndinu odziyesera nokha olungama pamaso pa anthu; koma Mulungu azindikira mitima yanu; chifukwa ichi chimene chikuzika mwa anthu chili chonyansa pamaso pa Mulungu.


Mfarisiyo anaimirira napemphera izi mwa yekha, Mulungu, ndikuyamikani kuti sindili monga anthu onse ena, opambapamba, osalungama, achigololo, kapenanso monga wamsonkho uyu;


Ndipo m'mene anachiona anadandaula onse, nanena, Analowa amchereze munthu ali wochimwa.


Koma Mfarisi, amene adamuitana Iye, pakuona, ananena mwa yekha, nati, Akadakhala mneneri uyu akadazindikira ali yani, ndi wotani mkaziyo womkhudza Iye, chifukwa ali wochimwa.


Ayuda anayankha nati kwa Iye, Kodi sitinenetsa kuti Inu ndinu Msamariya, ndipo muli ndi chiwanda?


Ndipo anamlalatira iye, nati, Ndiwe wophunzira wa Iyeyu, ife ndife ophunzira a Iyeyu, ife ndife ophunzira a Mose.


Anayankha nati kwa iye, Wabadwa iwe konse m'zoipa, ndipo iwe utiphunzitse ife kodi? Ndipo anamtaya kunja.


Ndipo anati kwa ine, Pita; chifukwa Ine ndidzakutuma iwe kunka kutali kwa amitundu.


Pakuti pakusadziwa chilungamo cha Mulungu, ndipo pofuna kukhazikitsa chilungamo cha iwo okha, iwo sanagonje ku chilungamo cha Mulungu.


Koma iwe uweruziranji mbale wako? Kapena iwenso upeputsiranji mbale wako? Pakuti ife tonse tidzaimirira kumpando wakuweruza wa Mulungu.


Wakudyayo asapeputse wosadyayo; ndipo wosadyayo asaweruze wakudyayo; pakuti Mulungu wamlandira.


Ndipo kale ine ndinali wamoyo popanda lamulo; koma pamene lamulo linadza, uchimo unatsitsimuka, ndipo ine ndinafa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa