Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 18:8 - Buku Lopatulika

8 Ndinena ndi inu, adzawachitira chilungamo posachedwa. Koma Mwana wa Munthu pakudza Iye, adzapeza chikhulupiriro padziko lapansi kodi?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndinena ndi inu, adzawachitira chilungamo posachedwa. Koma Mwana wa Munthu pakudza Iye, adzapeza chikhulupiriro pa dziko lapansi kodi?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Iyai, kunena zoona adzaŵaweruzira mlandu wao msanga. Komabe Mwana wa Munthu pobwera, kodi adzapezadi chikhulupiriro pansi pano?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Ine ndikukuwuzani inu, adzaonetsetsa kuti alandire chilungamo, ndiponso mofulumira. Komabe, pamene Mwana wa Munthu akubwera, kodi adzapeza chikhulupiriro pa dziko lapansi?”

Onani mutuwo Koperani




Luka 18:8
13 Mawu Ofanana  

Mulungu ali m'kati mwake, sudzasunthika, Mulungu adzauthandiza mbandakucha.


Anthu ambiri abukitsa yense kukoma mtima kwake; koma ndani angapeze munthu wokhulupirika?


Bwanji iwe, Yakobo, umati, ndi bwanji umanena iwe, Israele, Njira yanga yabisika kwa Yehova; ndipo chiweruzo cha Mulungu wanga chandipitirira?


chifukwa Akhristu onama adzauka, ndi aneneri onama nadzaonetsa zizindikiro zazikulu ndi zozizwa: kotero kuti akanyenge, ngati nkotheka, osankhidwa omwe. Onani ndakuuziranitu pasadafike.


Ndipo Yesu ananena kwa iye, Ankhandwe ali nazo nkhwimba zao, ndi mbalame za m'mlengalenga zisa zao, koma Mwana wa Munthu alibe potsamira mutu wake.


Ndipo m'chisiriro adzakuyesani malonda ndi mau onyenga; amene chiweruzo chao sichinachedwe ndi kale lomwe, ndipo chitayiko chao sichiodzera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa