Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 17:25 - Buku Lopatulika

25 Koma ayenera ayambe wamva zowawa zambiri nakanidwe ndi mbadwo uno.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Koma ayenera athange wamva zowawa zambiri nakanidwe ndi mbadwo uno.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Koma Iye ayenera kuti ayambe wamva zoŵaŵa zambiri, ndipo kuti anthu amakono amkane.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Koma poyamba ayenera kuzunzika mu zambiri ndi kukanidwa ndi mʼbado uno.

Onani mutuwo Koperani




Luka 17:25
18 Mawu Ofanana  

Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu; munthu wazisoni, ndi wodziwa zowawa; ndipo ananyozedwa monga munthu wombisira anthu nkhope zao; ndipo ife sitinamlemekeze.


Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kuwalangiza ophunzira ake, kuti kuyenera Iye amuke ku Yerusalemu, kukazunzidwa zambiri ndi akulu, ndi ansembe aakulu, ndi alembi; ndi kukaphedwa, ndi tsiku lachitatu kuuka kwa akufa.


Yesu ananena kwa iwo, Kodi simunawerenge konse m'malembo, Mwala umene anaukana omanga nyumba womwewu unakhala mutu wa pangodya: Ichi chinachokera kwa Ambuye, ndipo chili chozizwitsa m'maso mwathu?


nati, Taonani, tikwera ku Yerusalemu; ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kwa ansembe aakulu ndi alembi; ndipo iwo adzamweruza kuti ayenera imfa, nadzampereka Iye kwa anthu a mitundu;


Kodi simunawerenge ngakhale lembo ili, Mwala umene anaukana omanga nyumba, womwewu unayesedwa mutu wa pangodya:


Ndipo anayamba kuwaphunzitsa, kuti kuyenera kuti Mwana wa Munthu akamve zowawa zambiri, nakakanidwe ndi akulu ndi ansembe aakulu, ndi alembi, nakaphedwe, ndipo mkucha wake akauke.


Pakuti anaphunzitsa ophunzira ake, nanena nao, kuti, Mwana wa Munthu aperekedwa m'manja anthu, ndipo adzamupha Iye; ndipo ataphedwa, adzauka pofika masiku atatu.


Ndipo anadzitengera khumi ndi awiriwo, nati kwa iwo, Taonani, tikwera kunka ku Yerusalemu, ndipo zidzakwaniritsidwa kwa Mwana wa Munthu zonse zolembedwa ndi aneneri.


ndipo atamkwapula adzamupha Iye; ndipo tsiku lachitatu adzauka.


ndipo anati kwa iwo, Kotero kwalembedwa, kuti Khristu amve zowawa, nauke kwa akufa tsiku lachitatu;


nati, Kuyenera kuti Mwana wa Munthu amve zowawa zambiri, ndi kukanidwa ndi akulu, ndi ansembe aakulu, ndi alembi, ndi kuphedwa, ndi kuuka tsiku lachitatu.


Anadza kwa zake za Iye yekha, ndipo ake a mwini yekha sanamlandire Iye.


kuti mau a Yesaya mneneri akakwaniridwe, amene anati, Ambuye, wakhulupirira ndani kulalikira kwathu? Ndipo mkono wa Ambuye wavumbulutsidwa kwa yani?


koma lero inu mwakana Mulungu wanu amene anakupulumutsani yekha m'matsoka anu onse, ndi m'masautso anu; ndipo munanena naye, Koma mutipatse mfumu. Chifukwa chake tsono mudzionetse pamaso pa Yehova mafukomafuko, ndi magulumagulu.


Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Umvere mau onse anthuwo alikulankhula nawe; popeza sindiwe anakukana, koma ndine anandikana, kuti ndisakhale mfumu yao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa