Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 17:24 - Buku Lopatulika

24 pakuti monga mphezi ing'anipa kuchokera kwina pansi pa thambo, niunikira kufikira kwina pansi pa thambo, kotero adzakhala Mwana wa Munthu m'tsiku lake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 pakuti monga mphezi ing'anipa kuchokera kwina pansi pa thambo, niunikira kufikira kwina pansi pa thambo, kotero adzakhala Mwana wa Munthu m'tsiku lake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Pajatu monga mphezi imang'anipa nkuŵala kuchokera mbali ina ya kuthambo kufikira mbali yake ina, Mwana wa Munthu adzateronso pa tsiku la kubwera kwake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Pakuti monga mphenzi ingʼanima ndi kuwala kuchokera mbali ina ya thambo kufikira inzake, koteronso adzakhala ali Mwana wa Munthu pa tsiku lake.

Onani mutuwo Koperani




Luka 17:24
16 Mawu Ofanana  

Ndipo zamoyozo zinathamanga ndi kubwerera, ngati maonekedwe a mphezi yong'anima.


Ndipo Yehova adzaoneka pamwamba pao, ndi muvi wake udzatuluka ngati mphezi; ndipo Ambuye Mulungu adzaomba lipenga, nadzayenda ndi akamvulumvulu a kumwera.


Pakuti monga mphezi idzera kum'mawa, nionekera kufikira kumadzulo; kotero kudzakhalanso kufika kwake kwa Mwana wa Munthu.


ndipo pomwepo padzaoneka m'thambo chizindikiro cha Mwana wa Munthu; ndipo mitundu yonse ya padziko lapansi idzadziguguda pachifuwa, nidzapenya Mwana wa Munthu alinkudza pa mitambo ya kumwamba, ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.


Koma pamene Mwana wa Munthu adzadza mu ulemerero wake, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo Iye adzakhala pa chimpando cha kuwala kwake:


Yesu anati kwa iye, Mwatero, koma ndinenanso kwa inu, Kuyambira tsopano mudzaona Mwana wa Munthu ali kukhala kudzanja lamanja la mphamvu, ndi kufika pa mitambo ya kumwamba.


Kapena sayatsa nyali, ndi kuivundikira m'mbiya, koma aiika iyo pa choikapo chake; ndipo iunikira onse ali m'nyumbamo.


amenenso adzakukhazikitsani inu kufikira chimaliziro, kuti mukhale opanda chifukwa m'tsiku la Ambuye wathu Yesu Khristu.


Pakuti inu nokha mudziwa bwino kuti tsiku la Ambuye lidzadza monga mbala usiku.


kuti musamagwedezeka mtima msanga ndi kutaya maganizo anu, kapena kuopsedwa, mwa mzimu kapena mwa mau; kapena mwa kalata, monga wolembedwa ndi ife, monga ngati tsiku la Ambuye lafika;


Ndipo pamenepo adzavumbulutsidwa wosaweruzikayo, amene Ambuye Yesu adzamthera ndi mzimu wa pakamwa pake, nadzamuononga ndi maonekedwe a kudza kwake;


Lezani mtima inunso, limbitsani mitima yanu; pakuti kudza kwake kwa Ambuye kuyandikira.


Koma tsiku la Ambuye lidzadza ngati mbala; m'mene miyamba idzapita ndi chibumo chachikulu, ndi zam'mwamba zidzakanganuka ndi kutentha kwakukulu, ndipo dziko ndi ntchito zili momwemo zidzatenthedwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa