Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 12:57 - Buku Lopatulika

57 Ndipo inunso, pa nokha mulekeranji kuweruza kolungama?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

57 Ndipo inunso, pa nokha mulekeranji kuweruza kolungama?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

57 “Bwanji simutsimikiza nokha zoyenera kuchita?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

57 “Bwanji simukuzindikira nokha zoyenera kuchita?

Onani mutuwo Koperani




Luka 12:57
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Indedi ndinena kwa inu, Ngati mukhala nacho chikhulupiriro, osakayikakayika, mudzachita si ichi cha pa mkuyu chokha, koma ngati mudzati ngakhale kuphiri ili, Tanyamulidwa, nuponyedwe m'nyanja, chidzachitidwa.


Popeza Yohane anadza kwa inu m'njira ya chilungamo, ndipo simunamvere iye; koma amisonkho ndi akazi achiwerewere anammvera iye; ndipo inu, m'mene munachiona, simunalape pambuyo pake, kuti mumvere iye.


pamene iphukira, muipenya nimuzindikira pa nokha kuti dzinja lili pafupi pomwepo.


Musaweruze monga maonekedwe, koma weruzani chiweruziro cholungama.


Ndipo ndi mau ena ambiri anachita umboni, nawadandaulira iwo, nanena, Mudzipulumutse kwa mbadwo uno wokhotakhota.


Lingirirani mwa inu nokha: Kodi nkuyenera kuti apemphere kwa Mulungu, wosafunda mutu?


Kodi ubadwidwe womwe sutiphunzitsa kuti ngati mwamuna aweta tsitsi chinyozetsa iye?


Akadakhala nazo nzeru, akadazindikira ichi, akadasamalira chitsirizo chao!


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa