Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Luka 12:58 - Buku Lopatulika

58 Pakuti pamene ulikupita naye mnzako wa mlandu kwa oweruza, fulumira panjira kutha naye mlandu, kuti angakokere iwe kwa oweruza, ndipo oweruzayo angapereke iwe kwa msilikali, ndi msilikali angaponye iwe m'nyumba yandende.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

58 Pakuti pamene ulikupita naye mnzako wa mlandu kwa oweruza, fulumira panjira kutha naye mlandu, kuti angakokere iwe kwa oweruza, ndipo oweruzayo angapereke iwe kwa msilikali, ndi msilikali angaponye iwe m'nyumba yandende.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

58 Monga pamene ukupita ndi mnzako wamlandu kwa woweruza, uyesetse kukonza mlanduwo mukali pa njira, kuwopa kuti angakupereke kwa woweruza, woweruzayo angakakupereke kwa msilikali, ndipo msilikaliyo angakakuponye m'ndende.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

58 Pamene mukupita kwa woweruza ndi amene munalakwirana naye, yesetsani kwambiri kuti muyanjane naye mʼnjiramo, chifukwa mukapanda kutero akhoza kukutengerani ku bwalo la milandu ndipo woweruzayo adzakuperekani kwa woyangʼanira ndende, ndipo woyangʼanira ndendeyo adzakuponyani mʼndende.

Onani mutuwo Koperani




Luka 12:58
20 Mawu Ofanana  

Uzolowerane ndi Iye, nukhale ndi mtendere; ukatero zokoma zidzakudzera.


Apo woongoka mtima akadatsutsana naye; ndipo ndikadapulumuka chipulumukire kwa Woweruza wanga.


Chifukwa chake oyera mtima onse apemphere kwa Inu, pa nthawi ya kupeza Inu; indetu pakusefuka madzi aakulu sadzamfikira iye.


Dziwitsani ichi inu oiwala Mulungu, kuti ndingakumwetuleni, ndipo mungasowepo mpulumutsi.


Funani Yehova popezeka Iye, itanani Iye pamene ali pafupi;


Ndipo iye sanafune; koma anamuka, namponya iye m'nyumba yandende, kufikira abwezere ngongole.


(pakuti anena, M'nyengo yolandiridwa ndinamva iwe, ndipo m'tsiku la chipulumutso ndinakuthandiza. Taonani, tsopano ndiyo nyengo yabwino yolandiridwa, taonani, tsopano ndilo tsiku la chipulumutso);


m'menemonso anapita, nalalikira mizimu inali m'ndende,


Koma ndidzachitanso changu kosalekeza kuti nditachoka ine, mudzakhoza kukumbukira izi.


Okondedwa, pakuchita changu chonse chakukulemberani za chipulumutso cha ife tonse, ndafulumidwa mtima ine kukulemberani ndi kudandaulira kuti mulimbanetu chifukwa cha chikhulupiriro chapatsidwa kamodzi kwa oyera mtima.


Ndipo pamene zidzatha zaka chikwi, adzamasulidwa Satana m'ndende yake;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa