Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 12:1 - Buku Lopatulika

1 Pomwepo pamene anthu a zikwizikwi a khamu anasonkhana pamodzi, kotero kuti anapondana, Iye anayamba kunena kwa ophunzira ake poyamba, Tachenjerani nokha ndi chotupitsa mikate cha Afarisi, chimene chili chinyengo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Pomwepo pamene anthu a zikwizikwi a khamu anasonkhana pamodzi, kotero kuti anapondana, Iye anayamba kunena kwa ophunzira ake poyamba, Tachenjerani nokha ndi chotupitsa mikate cha Afarisi, chimene chili chinyengo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Nthaŵi imeneyo nkuti chikhamu cha anthu zikwi ndi zikwi chikusonkhana, kotero kuti anthuwo ankangopondana. Yesu adayamba kulankhula ndi ophunzira ake poyamba, Adati, “Chenjerani ndi chofufumitsira buledi cha Afarisi, chimene chili chiphamaso.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Nthawi yomweyo, anthu miyandamiyanda atasonkhana, ndi kumapondanapondana, Yesu anayamba kuyankhula poyamba kwa ophunzira ake, nati, “Chenjereni ndi yisiti wa Afarisi, amene ndi chinyengo.

Onani mutuwo Koperani




Luka 12:1
18 Mawu Ofanana  

Koma mfumu idayang'anitsa pachipata kazembe amene uja idafotsamira padzanja lake; ndipo anthu anampondereza pachipata, nafa iye, monga umo adanenera munthu wa Mulungu, ponena paja anamtsikira mfumu.


kuti kufuula kokondwera kwa woipa sikukhalira kutha, ndi chimwemwe cha wonyoza Mulungu chikhala kamphindi?


Pakuti chiyembekezo cha wonyoza Mulungu nchiyani pomlikhatu Mulungu, pomchotsera moyo wake?


Koma iwo a mtima wakunyoza Mulungu, akundika mkwiyo, akawamanga Iye, safuulira.


Ochimwa a mu Ziyoni ali ndi mantha, kunthunthumira kwadzidzimutsa anthu opanda Mulungu. Ndani mwa ife adzakhala ndi moto wakunyeketsa? Ndani mwa ife adzakhala ndi zotentha zachikhalire?


Tsoka inu! Chifukwa muli ngati manda osaoneka, ndipo anthu akuyendayenda pamwamba pao sadziwa.


Onyenga inu, mudziwa kuzindikira nkhope yake ya dziko lapansi ndi ya thambo; koma simudziwa bwanji kuzindikira nyengo ino?


Ndipo panali, pakumkanikiza khamu la anthu, kudzamva mau a Mulungu, Iye analikuimirira m'mbali mwa nyanja ya Genesarete;


Koma makamaka mbiri yake ya Iye inabuka: ndipo mipingo yambiri ya anthu inasonkhana kudzamvera, ndi kudzachiritsidwa nthenda zao.


Ndipo Iye anatsika nao, naima pachidikha, ndi khamu lalikulu la ophunzira ake, ndi unyinji waukulu wa anthu a ku Yudeya yense ndi Yerusalemu, ndi a ku mbali ya nyanja ya ku Tiro ndi Sidoni, amene anadza kudzamva Iye ndi kudzachiritsidwa nthenda zao;


Ndipo pamene anazimva, analemekeza Mulungu; nati kwa iye, Uona, mbale, kuti ambirimbiri mwa Ayuda akhulupirira; ndipo ali nacho changu onsewa, cha pa chilamulo;


Pakuti ndinapereka kwa inu poyamba, chimenenso ndinalandira, kuti Khristu anafera zoipa zathu, monga mwa malembo;


Komatu mwayandikira kuphiri la Ziyoni, ndi mzinda wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wa Kumwamba, ndi kwa unyinji wochuluka wa angelo,


Koma nzeru yochokera kumwamba iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomvera bwino, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankho, yosadzikometsera pamaso.


Momwemo pakutaya choipa chonse, ndi chinyengo chonse, ndi maonekedwe onyenga, ndi kaduka, ndi masinjiriro onse,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa