Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 11:49 - Buku Lopatulika

49 Mwa ichinso nzeru ya Mulungu inati, Ndidzatumiza kwa iwo aneneri ndi atumwi; ndipo ena a iwo adzawapha, nadzawazunza;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

49 Mwa ichinso nzeru ya Mulungu inati, Ndidzatumiza kwa iwo aneneri ndi atumwi; ndipo ena a iwo adzawapha, nadzawazunza;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

49 Nchifukwa chake Nzeru ya Mulungu idati, ‘Ndidzaŵatumizira aneneri ndi atumwi, koma anthu adzapha ena mwa iwo, nkuzunza ena.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

49 Chifukwa cha ichi, Mulungu mu nzeru zake anati, ‘Ine ndidzawatumizira aneneri ndi atumwi, ena mwa iwo adzawapha ndipo ena adzawazunza.’

Onani mutuwo Koperani




Luka 11:49
27 Mawu Ofanana  

Chiyambire tsiku limene makolo anu anatuluka m'dziko la Ejipito kufikira lero lino, ndatumiza kwa inu atumiki anga onse, aneneri, tsiku ndi tsiku, kuuka mamawa ndi kuwatumiza iwo;


ndipo otsala anagwira akapolo ake, nawachitira chipongwe, nawapha.


Chomwecho muli mboni, ndipo muvomera ntchito za makolo anu; chifukwa iwotu anawapha, koma inu muwamangira iwo zapamanda.


ndi kuti kulalikidwe m'dzina lake kulapa ndi kukhululukidwa kwa machimo kwa mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu.


Adzakutulutsani m'masunagoge, koma ikudza nthawi imene yense wakupha inu adzayesa kuti atumikira Mulungu.


Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ndi mu Yudeya monse, ndi mu Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.


Koma masiku awa aneneri anatsika ku Yerusalemu kudza ku Antiokeya.


ndipo pamene anakhetsa mwazi wa Stefano mboni yanu, ine ndemwe ndinalikuimirirako, ndi kuvomerezana nao, ndi kusunga zovala za iwo amene anamupha iye.


Koma anafuula ndi mau aakulu, natseka m'makutu mwao, namgumukira iye ndi mtima umodzi;


Ndipo Saulo anapasula Mpingo, nalowa nyumba ndi nyumba, nakokamo amuna ndi akazi, nawaika m'ndende.


koma kwa iwo oitanidwa, ndiwo Ayuda ndi Agriki, Khristu mphamvu ya Mulungu, ndi nzeru ya Mulungu.


Koma kwa Iye muli inu mwa Khristu Yesu, amene anayesedwa kwa ife nzeru ya kwa Mulungu, ndi chilungamo ndi chiyeretso ndi chiombolo;


Ndipo Iye anapatsa ena akhale atumwi; ndi ena aneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi;


amene zolemera zonse za nzeru ndi chidziwitso zibisika mwa Iye.


popeza anatsanulira mwazi wa oyera mtima, ndi wa aneneri, ndipo mudawapatsa mwazi amwe; ayenera iwo.


Kondwera pa iye, m'mwamba iwe, ndi oyera mtima, ndi atumwi, ndi aneneri inu; chifukwa Mulungu anauweruzira kuweruzidwa kwanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa