Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 11:48 - Buku Lopatulika

48 Chomwecho muli mboni, ndipo muvomera ntchito za makolo anu; chifukwa iwotu anawapha, koma inu muwamangira iwo zapamanda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

48 Chomwecho muli mboni, ndipo muvomera ntchito za makolo anu; chifukwa iwotu anawapha, koma inu muwamangira iwo zapamanda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

48 Apo mukutsimikiza kuti mukuvomereza ntchito za makolo anuwo, popeza kuti iwowo adapha aneneriwo, inuyo nkumamanga ziliza zao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

48 Tsono potero mumachitira umboni za zimene makolo anu anachita. Anapha aneneri, ndipo inu mumawaka manda awo.

Onani mutuwo Koperani




Luka 11:48
14 Mawu Ofanana  

koma ananyodola mithenga ya Mulungu, napeputsa mau ake, naseka aneneri ake, mpaka ukali wa Yehova unaukira anthu ake, mpaka panalibe cholanditsa.


Pakamwa pako pakutsutsa, si ine ai. Inde milomo yako ikuchitira umboni wakukutsutsa.


Adzawakhumudwitsa, lilime lao lidzawatsutsa; onse akuwaona adzawathawa.


Koma inu mukuti, Alekeranji mwana kusenza mphulupulu za atate wake? Mwanayo akachita chiweruzo ndi chilungamo, nakasunga malemba anga onse, ndi kuwachita, adzakhala ndi moyo ndithu.


Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mufanafana ndi manda opaka njereza, amene aonekera okoma kunja kwake, koma adzala m'katimo ndi mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zonse.


Pomwepo mutsimikiza nokha, kuti muli ana a iwo amene anapha aneneri.


Tsoka inu! Chifukwa mumanga za pa manda a aneneri, ndipo makolo anu anawapha.


Mwa ichinso nzeru ya Mulungu inati, Ndidzatumiza kwa iwo aneneri ndi atumwi; ndipo ena a iwo adzawapha, nadzawazunza;


amene ngakhale adziwa kuweruza kwake kwa Mulungu, kuti iwo amene achita zotere ayenera imfa, azichita iwo okha, ndiponso avomerezana ndi iwo akuzichita.


Tengani, abale, chitsanzo cha kumva zowawa ndi kuleza mtima, aneneri amene analankhula m'dzina la Ambuye.


Ndipo Yoswa ananena ndi anthu, Inu mwadzichitira mboni inu nokha kuti mwadzisankhira Yehova kumtumikira Iye. Ndipo anati, Ndife mboni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa