Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 11:45 - Buku Lopatulika

45 Ndipo mmodzi wa achilamulo anayankha, nanena kwa Iye, Mphunzitsi, ndi kunena izi, mutitonza ifenso.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

45 Ndipo mmodzi wa achilamulo anayankha, nanena kwa Iye, Mphunzitsi, ndi kunena izi, mutitonza ifenso.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

45 Apo katswiri wina wa Malamulo adati, “Aphunzitsi, mukamanena zimenezi, mukunyozatu ndi ife tomwe.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

45 Mmodzi mwa akatswiri a Malamulo anamuyankha Iye nati, “Aphunzitsi, pamene mukunena zinthu izi, mukutinyoza ifenso?”

Onani mutuwo Koperani




Luka 11:45
11 Mawu Ofanana  

Ndipo mfumu ya Israele inati kwa Yehosafati, Alipo munthu wina kuti tifunsire kwa Yehova mwa iye; koma ndimuda, popeza samanenera za ine zabwino, koma zoipa; ndiye Mikaya mwana wake wa Imila. Nati Yehosafati, Isamatero mfumu.


Pakuti paliponse ndinena, ndifuula; ndifuula, Chiwawa ndi chofunkha; pakuti mau a Yehova ayesedwa kwa ine chitonzo, ndi choseketsa, dzuwa lonse.


Ndidzanena ndi yani, ndidzachita mboni kwa yani, kuti amve? Taona khutu lao lili losadulidwa, ndipo sangathe kumva; taona, mau a Yehova awatonzetsa iwo; sakondwera nao.


Ndipo mmodzi wa iwo, mphunzitsi wa malamulo, anamfunsa ndi kumuyesa Iye, nati,


Ndipo anati, Tsoka inunso, achilamulo inu! Chifukwa musenzetsa anthu akatundu osautsa ponyamula, ndipo inu nomwe simukhudza akatunduwo ndi chala chanu chimodzi.


Tsoka inu, achilamulo! Chifukwa munachotsa chifungulo cha nzeru; inu simunalowamo nokha, ndipo munawaletsa iwo analinkulowa.


Koma Afarisi ndi achilamulo anakaniza uphungu wa Mulungu kwa iwo okha, popeza sanabatizidwe ndi iye.


Kodi wina wa akulu anakhulupirira Iye, kapena wa Afarisi?


Dziko lapansi silingathe kudana ndi inu; koma Ine lindida popeza Ine ndilichitira umboni, kuti ntchito zake zili zoipa.


Ndipo Afarisi ena akukhala ndi Iye anamva izi, nati kwa Iye, Kodi ifenso ndife osaona?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa