Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 11:22 - Buku Lopatulika

22 koma pamene paliponse amdzera wakumposa mphamvu, nakamgonjetsa, amchotsera zida zake zonse zimene anazitama, nagawa zofunkha zake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 koma pamene paliponse amdzera wakumposa mphamvu, nakamlaka, amchotsera zida zake zonse zimene anazitama, nagawa zofunkha zake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Koma pakabwera wina wamphamvu zoposa, namgonjetsa, amalanda zida zimene ankazidalirazo, nkugaŵagaŵa katundu amene walandayo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Koma pakabwera wina wamphamvu zoposa namugonjetsa, amalanda zida zimene munthuyo amazidalirazo ndi kugawa katundu wake.

Onani mutuwo Koperani




Luka 11:22
14 Mawu Ofanana  

ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitendeni chake.


Mdani anati, Ndiwalondola, ndiwapeza, ndidzagawa zofunkha; ndidzakhuta nao mtima; ndidzasolola lupanga langa, dzanja langa lidzawaononga.


Tsiku limenelo Yehova ndi lupanga lake lolimba ndi lalikulu ndi lamphamvu adzalanga Leviyatani njoka yothamanga, ndi Leviyatani njoka yopindikapindika; nadzapha ching'ona chimene chili m'nyanja.


Chifukwa chake ndidzamgawira gawo ndi akulu; ndipo adzagawana ndi amphamvu zofunkha; pakuti Iye anathira moyo wake kuimfa; ndipo anawerengedwa pamodzi ndi olakwa; koma ananyamula machimo a ambiri, napembedzera olakwa.


Pamene paliponse mwini mphamvu alonda pabwalo pake zinthu zake zili mumtendere;


Iye wosavomerezana ndi Ine atsutsana ndi Ine; ndipo iye wosasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amwaza.


Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchilimika pokana machenjerero a mdierekezi.


Mwa ichi mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoza kuima chitsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutachita zonse, mudzachilimika.


atavula maukulu ndi maulamuliro, anawaonetsera poyera, nawagonjetsera nako.


iye wochita tchimo ali wochokera mwa mdierekezi, chifukwa mdierekezi amachimwa kuyambira pachiyambi. Kukachita ichi Mwana wa Mulungu adaonekera, ndiko kuti akaononge ntchito za mdierekezi.


Inu ndinu ochokera mwa Mulungu, tiana, ndipo munaipambana; pakuti Iye wakukhala mwa inu aposa iye wakukhala m'dziko lapansi. Iwo ndiwo ochokera m'dziko lapansi;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa