Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 10:30 - Buku Lopatulika

30 Ndipo Yesu anamlanda mau, nati, Munthu wina anatsika kuchokera ku Yerusalemu kunka ku Yeriko; ndipo anagwa m'manja a achifwamba amene anamvula zovala, namkwapula, nachoka atamsiya wofuna kufa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 Ndipo Yesu anamlanda mau, nati, Munthu wina anatsika kuchokera ku Yerusalemu kunka ku Yeriko; ndipo anagwa m'manja a achifwamba amene anamvula zovala, namkwapula, nachoka atamsiya wofuna kufa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Apo Yesu adati, “Munthu wina ankatsikira ku Yeriko kuchokera ku Yerusalemu. Pa njira achifwamba adamgwira. Adamuvula zovala, nammenya, nkumusiya ali thasa, ali pafupi kufa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 Yesu pomuyankha anati, “Munthu wina ankatsikira ku Yeriko kuchokera ku Yerusalemu. Pa njira anavulazidwa ndi achifwamba. Anamuvula zovala zake, namumenya ndi kuthawa, namusiya ali pafupi kufa.

Onani mutuwo Koperani




Luka 10:30
7 Mawu Ofanana  

Anandiwerenga pamodzi nao otsikira kudzenje; ndakhala ngati munthu wopanda mphamvu.


Chifukwa chake, taona, masiku alinkudza, ati Yehova, amene ndidzaweruza mafano ake; ndipo padziko lake lonse olasidwa adzabuula.


Amati kwa amao, Tirigu ndi vinyo ali kuti? Pokomoka iwo ngati olasidwa m'makwalala a mzindawu, potsanulidwa miyoyo yao pa zifuwa za amao.


Ndipo ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babiloni, ndi kuika lupanga langa m'dzanja lake; koma ndidzathyola manja a Farao, ndipo adzabuula pamaso pake mabuulo a munthu wopyozedwa.


Ndipo kudangotero kuti wansembe wina anatsika njirayo, ndipo pakumuona iye anapita mbali ina.


Ndipo anadzitengera khumi ndi awiriwo, nati kwa iwo, Taonani, tikwera kunka ku Yerusalemu, ndipo zidzakwaniritsidwa kwa Mwana wa Munthu zonse zolembedwa ndi aneneri.


Ndipo m'mene adanena izi anawatsogolera nakwera ku Yerusalemu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa