Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 1:48 - Buku Lopatulika

48 chifukwa Iye anayang'anira umphawi wa mdzakazi wake; pakuti taonani, kuyambira tsopano, anthu a mibadwo yonse adzanditchula ine wodala.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

48 chifukwa Iye anayang'anira umphawi wa mdzakazi wake; pakuti taonani, kuyambira tsopano, anthu a mibadwo yonse adzanditchula ine wodala.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

48 popeza kuti wayang'ana kutsika kwa mtumiki wake. Ndithu kuyambira tsopano anthu a mibadwo yonse adzanditcha wodala,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

48 pakuti wakumbukira kudzichepetsa kwa mtumiki wake. Kuyambira tsopano mibado yonse idzanditcha wodala,

Onani mutuwo Koperani




Luka 1:48
19 Mawu Ofanana  

Ndipo Leya anati, Ndakondwa ine! Chifukwa kuti ana aakazi adzanditcha ine wokondwa: ndipo anamutcha dzina lake Asere.


Chifukwa chake tsono udzatero kwa mtumiki wanga Davide, Atero Yehova wa makamu, Ndinakuchotsa kubusako kumene unalikutsata nkhosa kuti udzakhale mfumu ya anthu anga, ndiwo Israele.


anasamalira pemphero la iwo akusowa konse, osapepula pemphero lao.


Amene anatikumbukira popepuka ife; pakuti chifundo chake nchosatha.


Angakhale Yehova ngwokwezeka, apenyanso wopepukayo; koma wodzikuza amdziwira kutali.


Dzina lake lidzakhala kosatha, momwe likhalira dzuwa dzina lake lidzamvekera zidzukulu. Ndipo anthu adzadalitsidwa mwa Iye; amitundu onse adzamutcha wodala.


Pakuti zonsezi mkono wanga wazilenga, momwemo zonsezi zinaoneka, ati Yehova; koma ndidzayang'anira munthu uyu amene ali waumphawi, ndi wa mzimu wosweka, nanthunthumira ndi mau anga.


Ndipo amitundu onse adzatcha inu odala; pakuti mudzakhala dziko lokondweretsa, ati Yehova wa makamu.


Ndipo pakulowa mngelo anati kwa iye, Tikuoneni, wochitidwa chisomo, Ambuye ali ndi iwe.


nakweza mau ndi mfuu waukulu, nati, Wodalitsika iwe mwa akazi, ndipo chodalitsika chipatso cha mimba yako.


Ndipo wodala ali iye amene anakhulupirira; chifukwa zidzachitidwa zinthu zimene Ambuye analankhula naye.


Chifukwa Iye Wamphamvuyo anandichitira ine zazikulu; ndipo dzina lake lili loyera.


Ndipo kunali, pakunena izi Iye, mkazi wina mwa khamu la anthu anakweza mau, nati kwa Iye, Yodala mimba imene idakubalani, ndi mawere amene munayamwa.


nalonjeza chowinda, nati, Yehova wa makamu, mukapenyera ndithu kusauka kwa mdzakazi wanu, ndi kukumbukira ine, ndi kusaiwala mdzakazi wanu, mukapatsa mdzakazi wanu mwana wamwamuna, ine ndidzampereka kwa Yehova masiku onse a moyo wake, ndipo palibe lumo lidzapita pamutu pake.


Amuutsa waumphawi m'fumbi, nanyamula wosowa padzala, kukamkhalitsa kwa akalonga; ndi kuti akhale nacho cholowa cha chimpando cha ulemerero. Chifukwa nsanamira za dziko lapansi nza Yehova, ndipo Iye anakhazika dziko pa izo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa