Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 9:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo ana a Aroni anasendera nao mwazi kwa iye; ndipo anaviika chala chake m'mwazimo naupaka pa nyanga za guwa la nsembe, nathira mwaziwo patsinde paguwa la nsembe;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo ana a Aroni anasendera nao mwazi kwa iye; ndipo anaviika chala chake m'mwazimo naupaka pa nyanga za guwa la nsembe, nathira mwaziwo patsinde pa guwa la nsembe;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Ndipo ana ake adapereka magazi kwa Aroni. Iyeyo adaviika chala chake m'magazimo, naŵapaka pa nyanga za guwa, nathira magaziwo patsinde pa guwa lomwelo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Ana a Aaroni anabwera ndi magazi kwa Aaroni ndipo iye anaviyika chala chake mʼmagaziwo, nawapaka pa nyanga za guwa. Magazi wotsalawo anawathira pa tsinde la guwalo.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 9:9
14 Mawu Ofanana  

Ndi guwa lapamwamba mikono inai; ndi pamoto paguwa padzatuluka nyanga zinai.


Nutengeko mwazi wake, ndi kupaka pa nyanga zinai za guwa, ndi pangodya zinai za phaka, ndi pa mkuzi wake pozungulira; motero uliyeretse ndi kulichitira chotetezera.


Ndipo atulukire guwa la nsembe lokhala pamaso pa Yehova ndi kulichitira chotetezera; natengeko mwazi wa ng'ombeyo, ndi mwazi wa mbuziyo, ndi kuupaka pa nyanga za guwa la nsembe pozungulira.


Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yauchimo ndi chala chake, nauike pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza, ndi kuthira mwazi wake patsinde pa guwa la nsembe yopsereza.


Ndipo wansembe atengeko mwazi ndi chala chake, nauike pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza, ndi kuthira mwazi wake wonse patsinde pa guwa la nsembe.


Ndipo anaipha; ndi Mose anatenga mwaziwo, naupaka ndi chala chake pa nyanga za guwa la nsembe pozungulira; nayeretsa guwa la nsembe, nathira mwazi patsinde paguwa la nsembe, nalipatula, kuti alichitire cholitetezera.


koma mafutawo, ndi impso, ndi chokuta cha mphafa za nsembe yauchimo, anazitentha paguwa la nsembe; monga Yehova analamula Mose.


Ndipo anapha nsembe yopsereza; ndi ana a Aroni anapereka mwaziwo kwa iye, ndipo anauwaza paguwa la nsembe pozungulira.


Anaphanso ng'ombe, ndi nkhosa yamphongoyo, ndizo nsembe zoyamika za anthu; ndi ana a Aroni anapereka kwa iye mwaziwo, ndipo anauwaza paguwa la nsembe pozungulira,


Pakuti kunamuyenera Iye amene zonse zili chifukwa cha Iye, ndi zonse mwa Iye, pakutenga ana ambiri alowe ulemerero, kumkonza wamphumphu mtsogoleri woyamba wa chipulumutso chao mwa zowawa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa