Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 9:10 - Buku Lopatulika

10 koma mafutawo, ndi impso, ndi chokuta cha mphafa za nsembe yauchimo, anazitentha paguwa la nsembe; monga Yehova analamula Mose.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 koma mafutawo, ndi impso, ndi chokuta cha mphafa za nsembe yauchimo, anazitentha pa guwa la nsembe; monga Yehova anauza Mose.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Koma mafuta ndi imso, pamodzi ndi mphumphu ya mafuta akuchiŵindi, za nsembe yopepesera machimoyo, adazitenthera pa guwa, monga momwe Chauta adaalamulira Mose.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Kenaka anatentha paguwapo, mafuta, impsyo pamodzi ndi mafuta amene amakuta chiwindi ngati nsembe yopepesera machimoyo, monga momwe Yehova analamulira Mose.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 9:10
13 Mawu Ofanana  

Nsembe za Mulungu ndizo mzimu wosweka; Inu, Mulungu, simudzaupeputsa mtima wosweka ndi wolapa.


Nutenge mafuta onse akukuta matumbo, ndi chokuta cha mphafa ndi impso ziwiri, ndi mafuta ali pa izo, ndi kuzitentha paguwa la nsembe.


Mwananga, undipatse mtima wako, maso ako akondwere ndi njira zanga.


Koma kunakomera Yehova kumtundudza; anammvetsa zowawa; moyo wake ukapereka nsembe yopalamula, Iye adzaona mbeu yake, adzatanimphitsa masiku ake; ndipo chomkondweretsa Yehova chidzakula m'manja mwake.


Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo aatali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.


Pakuti zonsezi mkono wanga wazilenga, momwemo zonsezi zinaoneka, ati Yehova; koma ndidzayang'anira munthu uyu amene ali waumphawi, ndi wa mzimu wosweka, nanthunthumira ndi mau anga.


Ndipo anatentha ndi moto nyamayi ndi chikopa kunja kwa chigono.


Ndipo ana a Aroni anasendera nao mwazi kwa iye; ndipo anaviika chala chake m'mwazimo naupaka pa nyanga za guwa la nsembe, nathira mwaziwo patsinde paguwa la nsembe;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa