Levitiko 9:7 - Buku Lopatulika7 Ndipo Mose anati kwa Aroni, Sendera kufupi kwa guwa la nsembe, nukonze nsembe yako yauchimo, ndi nsembe yako yopsereza, nudzichitire wekha ndi anthuwo chotetezera; nupereke chopereka cha anthu, ndi kuwachitira chotetezera; monga Yehova analamula. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Ndipo Mose anati kwa Aroni, Sendera kufupi kwa guwa la nsembe, nukonze nsembe yako yauchimo, ndi nsembe yako yopsereza, nudzichitire wekha ndi anthuwo chotetezera; nupereke chopereka cha anthu, ndi kuwachitira chotetezera; monga Yehova anauza. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Pamenepo Moseyo adauza Aroni kuti, “Sendera pafupi ndi guwa, ndipo upereke nsembe yopepesera machimo ndi nsembe yopsereza, kuti uchite mwambo wopepesera machimo ako ndi machimo a Aisraele. Ubwere ndi zopereka za anthuwo ndipo uchite mwambo wopepesera machimo ao, monga momwe Chauta walamulira.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 Pambuyo pake Mose anawuza Aaroni kuti, “Sendera pafupi ndi guwa ndipo upereka nsembe yako yopepesera machimo ndi nsembe yako yopsereza ndikuchita mwambo wopepesera machimo ako ndi machimo a anthu. Anthuwa apereke nsembe zawo zopepesera machimo monga momwe Yehova walamulira.” Onani mutuwo |