Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 9:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo Mose anati, Ichi ndi chimene Yehova anakuuzani kuti muchichite; ndipo ulemerero wa Yehova udzaonekera kwa inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo Mose anati, Ichi ndi chimene Yehova anakuuzani kuti muchichite; ndipo ulemerero wa Yehova udzaonekera kwa inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Apo Mose adati, “Nazi zimene Chauta akukulamulani kuti muchite, kuti ulemerero wake ukuwonekereni.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Tsono Mose anati, “Izi ndi zimene Yehova walamula kuti muchite kuti ulemerero wa Yehova ukuonekereni.”

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 9:6
9 Mawu Ofanana  

Ndipo kunakhala, pakunena Aroni ndi khamu lonse la ana a Israele kuti iwo anatembenukira kuchipululu, ndipo, taonani, ulemerero wa Yehova unaoneka mumtambo.


Ndipo ulemerero wa Yehova unakhalabe paphiri la Sinai, ndi mtambo unaliphimba masiku asanu ndi limodzi; ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri Iye ali m'kati mwa mtambo anaitana Mose.


Ndipo pamenepo ndidzakomana ndi ana a Israele; ndipo chihema chidzapatulidwa ndi ulemerero wanga.


ndipo taonani, ulemerero wa Mulungu wa Israele unadzera njira ya kum'mawa, ndi mau ake ananga mkokomo wa madzi ambiri, ndi dziko linanyezimira ndi ulemerero wake.


Ndipo Mose ndi Aroni analowa ku chihema chokomanako, natuluka, nadalitsa anthu; ndipo ulemerero wa Yehova unaonekera kwa anthu onse.


Pamenepo anatenga zimene Mose anawauza, napita nazo pakhomo pa chihema chokomanako; ndi msonkhano wonse unasendera kufupi nuimirira pamaso pa Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa