Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 8:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo anamveka ndi malaya a m'kati, nammanga m'chuuno ndi mpango, namveka ndi mwinjiro, namveka ndi efodi, nammanga m'chuuno ndi mpango wa efodi nammanga nao pathupi pake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo anamveka ndi malaya a m'kati, nammanga m'chuuno ndi mpango, namveka ndi mwinjiro, namveka ndi efodi, nammanga m'chuuno ndi mpango wa efodi nammanga nao pathupi pake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Kenaka adamuveka mwinjiro Aroniyo, ndi kummanga lamba m'chiwuno. Adamuveka mkanjo ndi chovala cha efodi, ndipo adammanganso lamba wa efodiyo m'chiwuno.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Anamuveka Aaroni mwinjiro, ndi kumumanga lamba mʼchiwuno. Anamuvekanso mkanjo wa efodi ndi efodiyo. Anamangira lamba efodiyo amene analukidwa mwaluso uja, motero efodiyo analimba mʼchiwunomo.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 8:7
12 Mawu Ofanana  

Ndipo usokere Aroni mbale wako zovala zopatulika, zikhale zaulemerero ndi zokoma.


Ndipo zovala azisoka ndi izi: chapachifuwa ndi efodi, ndi mwinjiro, ndi malaya opikapika, ndi nduwira, ndi mpango; tero apangire Aroni mbale wako ndi ana ake zovala zopatulika, kuti andichitire Ine ntchito ya nsembe.


Naombe efodi ndi golide, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya mmisiri.


Pamenepo utenge zovalazo ndi kuveka Aroni malaya am'kati, ndi mwinjiro wa efodi, ndi efodi, ndi chapachifuwa, ndi kummangira m'chuuno ndi mpango wa efodi woluka mwanzeru;


Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga; pakuti Iye wandiveka ine ndi zovala za chipulumutso, nandifunda chofunda cha chilungamo, monga mkwati avala nduwira, ndi monga mkwatibwi adzikometsa yekha ndi miyala yamtengo.


ndikakonzere iwo amene alira maliro mu Ziyoni, ndi kuwapatsa chovala kokometsa m'malo mwa phulusa, mafuta akukondwa m'malo mwa maliro, chovala cha matamando m'malo mwa mzimu wopsinjika; kuti iwo atchedwe mitengo ya chilungamo yakuioka Yehova, kuti Iye alemekezedwe.


Atalowa ansembe asatulukenso m'malo opatulika kunka kubwalo lakunja, koma komweko aziika zovala zao zimene atumikira nazo; pakuti zili zopatulika; ndipo avale zovala zina, nayandikire zinthu wamba za anthu.


Koma valani inu Ambuye Yesu Khristu, ndipo musaganizire za thupi kuchita zofuna zake.


ndicho chilungamo cha Mulungu chimene chichokera mwa chikhulupiriro cha pa Yesu Khristu kwa onse amene akhulupirira; pakuti palibe kusiyana;


Pakuti nonse amene munabatizidwa kwa Khristu mudavala Khristu.


Kodi sindinasankhule iye pakati pa mafuko onse a Israele, akhale wansembe wanga, kuti apereke nsembe paguwa langa, nafukize zonunkhira, navale efodi pamaso panga? Kodi sindinapatse banja la kholo lako zopereka zonse za kumoto za ana a Israele?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa