Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 7:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo nsembe zaufa zonse zophika mumchembo, ndi zonse zokonzeka mumphika, ndi pachiwaya, zikhale za wansembe amene wabwera nazo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo nsembe zaufa zonse zophika mumchembo, ndi zonse zokonzeka mumphika, ndi pachiwaya, zikhale za wansembe amene wabwera nazo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Tsono chopereka chilichonse cha chakudya chophika mu uvuni, kapena cha zonse zimene amakazinga mu mphika kapena m'chiwaya, zikhale za wansembe amene apereke zimenezo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Chopereka chilichonse cha chakudya chophika mu uvuni kapena chokazinga mu mʼphika kapena mu chiwaya ndi cha wansembe amene wapereka nsembezo.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 7:9
12 Mawu Ofanana  

Pamenepo Hazaele mfumu ya Aramu anakwera, nathira nkhondo pa Gati, naulanda, nalunjikitsa nkhope yake kukwera ku Yerusalemu.


Azidya nsembe yaufa, ndi nsembe yauchimo, ndi nsembe yopalamula; ndipo zilizonse zoperekedwa chiperekere mu Israele ndi zao.


Ndipo chotsalira cha nsembe yaufa chikhale cha Aroni ndi ana ake; ndicho chopatulika kwambiri cha nsembe zamoto za Yehova.


Ndipo wansembe amchitire chomtetezera chifukwa cha kuchimwa kwake adachimwira chimodzi cha izi, ndipo adzakhululukidwa; ndipo chotsalira chikhale cha wansembe, monga umo amachitira chopereka chaufacho.


Ndipo nsembe zonse zaufa zosakaniza ndi mafuta, kapena zouma zikhale za ana onse a Aroni, alandireko onse.


Ndipo chikopa cha nsembe yopsereza chikhale chakechake cha wansembe, amene anabwera nayo nsembe yopsereza ya munthu aliyense.


Izi ndi zako pa zinthu zopatulika kwambiri, zosafika kumoto; zopereka zao zonse, ndi nsembe zao zonse zaufa, ndi nsembe zao zonse zauchimo, ndi nsembe zao zonse zopalamula, zimene andibwezera Ine, zikhale zopatulika kwambiri za iwe ndi za ana ako aamuna.


Kodi simudziwa kuti iwo akutumikira za Kachisi amadya za mu Kachisi, ndi iwo akuimirira guwa la nsembe, agawana nalo guwa la nsembe?


Msilikali ndani achita nkhondo, nthawi iliyonse, nadzifunira zake yekha? Aoka mipesa ndani, osadya chipatso chake? Kapena aweta gulu ndani, osadya mkaka wake wa gululo? Kodi ndilankhula izi monga mwa anthu?


Koma iye amene aphunzira mau, ayenera kuchereza womphunzitsayo m'zonse zabwino.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa