Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 3:16 - Buku Lopatulika

16 Ndipo wansembe atenthe izi paguwa la nsembe; ndizo chakudya cha nsembe yamoto ichite fungo lokoma; mafuta onse nga Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo wansembe atenthe izi pa guwa la nsembe; ndizo chakudya cha nsembe yamoto ichite fungo lokoma; mafuta onse nga Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Wansembe atenthe zonsezo pa guwa, kuti zikhale chakudya chotentha pa moto, cha fungo lokoma. Mafuta onse nga Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Wansembe awotche zonsezi pa guwa. Ichi ndi chakudya cha Yehova, chowotcha pa moto ndiponso cha fungo lokomera Yehova. Mafuta onse ndi a Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 3:16
19 Mawu Ofanana  

Ndiponso Abele anatenga iyenso mwana woyamba wa nkhosa zake ndi mafuta omwe. Yehova ndipo anayang'anira Abele ndi nsembe yake:


Ndiponso zidachuluka nsembe zopsereza, pamodzi ndi mafuta a nsembe zamtendere, ndi nsembe zothira za nsembe yopsereza iliyonse. Momwemo utumiki wa nyumba ya Yehova unalongosoka.


Ndipo Solomoni anapatula pakati pake pa bwalo lili pakhomo pa nyumba ya Yehova; pakuti anapereka nsembe zopsereza, ndi mafuta a nsembe zoyamika pomwepo; popeza guwa la nsembe lamkuwa adalipanga Solomoni linachepa kulandira nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa, ndi mafuta.


Nutenge mafuta onse akukuta matumbo, ndi chokuta cha mphafa ndi impso ziwiri, ndi mafuta ali pa izo, ndi kuzitentha paguwa la nsembe.


Utengenso mafuta a nkhosa yamphongoyo, ndi mchira, chokuta cha mphafa, ndi impso ziwiri, ndi mafuta ali pamenepo, ndi mwendo wam'mwamba wa ku dzanja lamanja; pakuti ndiyo nkhosa yamphongo ya kudzaza manja;


Koma kunakomera Yehova kumtundudza; anammvetsa zowawa; moyo wake ukapereka nsembe yopalamula, Iye adzaona mbeu yake, adzatanimphitsa masiku ake; ndipo chomkondweretsa Yehova chidzakula m'manja mwake.


Koma ansembe Alevi, ana a Zadoki, akusunga udikiro wa malo anga opatulika pondisokerera ana a Israele, iwowa adzandiyandikira kunditumikira Ine, nadzaima pamaso panga, kupereka mafuta ndi mwazi kwa Ine, ati Ambuye Yehova;


Ndipo wansembeyo awaze mwaziwo paguwa la nsembe la Yehova, pa khomo la chihema chokomanako, natenthe mafuta akhale fungo lokoma lokwera kwa Yehova.


Ndipo atenthe mafuta ake onse paguwa la nsembe, monga mafuta a nsembe yoyamika; ndipo wansembe amchitire chomtetezera, ndipo adzakhululukidwa.


Nachotse mafuta ake onse, monga umo amachotsera mafuta pa nsembe yoyamika; ndipo wansembeyo awatenthe paguwa la nsembe akhale fungo lokoma la kwa Yehova; ndi wansembe amchitire chomtetezera, ndipo adzakhululukidwa.


Ndipo anatenga mafutawo ndi mchira wamafuta, ndi mafuta onse a pamatumbo, ndi chokuta cha mphafa, ndi impso ziwiri, ndi mafuta ake, ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja;


Ndipo unatuluka moto pamaso ya Yehova, nunyeketsa nsembe yopsereza ndi mafuta paguwa la nsembe; ndipo pakuchiona anthu onse anafuula, nagwa nkhope zao pansi.


Ndipo Yesu anati kwa iye, Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa