Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 22:9 - Buku Lopatulika

9 Potero asunge chilangizo changa, angasenzepo uchimo, ndi kufera m'mwemo, pakuchiipsa; Ine ndine Yehova wakuwapatula iwo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Potero asunge chilangizo changa, angasenzepo uchimo, ndi kufera m'mwemo, pakuchiipsa; Ine ndine Yehova wakuwapatula iwo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Nchifukwa chake ansembe asunge malamulo anga kuti angachimwe ndipo angafe chifukwa choŵaphwanya. Ine ndine Chauta, amene ndimaŵayeretsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 “ ‘Choncho ansembe azisunga malamulo angawa kuti asapezeke wolakwa ndi kufa chifukwa chopeputsa malamulowa. Ine ndine Yehova, amene ndimawayeretsa.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 22:9
10 Mawu Ofanana  

Ndipo azivale Aroni ndi ana ake, pakulowa iwo ku chihema chokomanako, kapena poyandikiza iwo kuguwa la nsembe kutumikira m'malo opatulika; anganyamule mphulupulu, nangafe; likhale lemba losatha la iye ndi mbumba zake pambuyo pake.


naike chofukizacho pamoto pamaso pa Yehova, kuti mtambo wa chofukiza chiphimbe chotetezerapo chokhala pamboni, kuti angafe.


ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni mbale wako, kuti asalowe nthawi zonse m'malo opatulika m'tseri mwa nsalu yotchinga, pali chotetezerapo chokhala palikasa, kuti angafe; popeza ndioneka mumtambo pachotetezerapo.


Potero muzisunga chilangizo changa, ndi kusachita zilizonse za miyambo yonyansayi anaichita musanafike inu, ndi kusadzidetsa nayo: Ine ndine Yehova Mulungu wako.


ndi kuwasenzetsa mphulupulu yakuwapalamulitsa, pakudya iwo zopatulika zao; pakuti Ine ndine Yehova wakuwapatula.


Ndipo kuyambira tsopano ana a Israele asayandikize chihema chokomanako, angamasenze uchimo kuti angafe.


Ndipo simudzasenzapo uchimo, mutakwezako zokometsetsa zake; ndipo musamaipsa zinthu zopatulika za ana a Israele, kuti mungafe.


Inu opusa, ndi akhungu: pakuti choposa nchiti, golide kodi, kapena Kachisi amene ayeretsa golideyo?


Chifukwa chake muzikonda Yehova Mulungu wanu, ndi kusunga chilangizo chake, ndi malemba ake, ndi maweruzo ake, ndi malamulo ake, masiku onse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa