Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 22:10 - Buku Lopatulika

10 Mlendo asadyeko chopatulikacho; wakungokhala, ndi wansembe, kapena wolembedwa ntchito, asadyeko chopatulikacho.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Mlendo asadyeko chopatulikacho; wakungokhala, ndi wansembe, kapena wolembedwa ntchito, asadyeko chopatulikacho.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 “Wapadera asadyeko zinthu zopatulika. Mlendo wongokhala nao kwa wansembe, kapena wantchito wake, asadyeko chinthu chopatulika.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 “ ‘Aliyense amene si wabanja la wansembe, kaya ndi mlendo wa wansembe, kapena wantchito wake, asadye chopereka chopatulika.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 22:10
11 Mawu Ofanana  

Ndipo kazembe anawauza kuti asadyeko zopatulika kwambiri, mpaka adzabuka wansembe wokhala ndi Urimu ndi Tumimu.


Ndipo Yehova anati kwa Mose ndi Aroni, Lemba la Paska ndi ili: mwana wa mlendo aliyense asadyeko;


Mlendo kapena wolembedwa ntchito asadyeko.


Ndipo adye zimene anachita nazo choteteza, kuti awadzaze manja ndi kuwapatulitsa; koma mlendo asadyeko, pakuti nzopatulika izi.


Ndipo simunasunge udikiro wa zopatulika zanga, koma mwadziikira nokha osunga udikiro wanga m'malo anga opatulika.


Adye chakudya cha Mulungu wake, chopatulika kwambiri, ndi chopatulika;


Koma mwana wamkazi wa wansembe akakhala wamasiye kapena wochotsedwa, ndipo alibe mwana, nabwerera kunyumba ya atate wake, monga muja anali mwana, adyeko mkate wa atate wake; koma mlendo asamadyako.


Koma uike Aroni ndi ana ake aamuna, azisunga ntchito yao ya nsembe; ndi mlendo wakusendera pafupi amuphe.


Kuti analowa m'nyumba ya Mulungu, nadya mikate yoonetsa, imene yosaloleka kudya iye kapena amene anali naye, koma ansembe okhaokha.


Chomwecho wansembeyo anampatsa mkate wopatulika, popeza panalibe mkate wina, koma mkate woonekera, umene adauchotsa pamaso pa Yehova, kuti akaike mkate wotentha tsiku lomwelo anachotsa winawo.


Tsono munthu wina wa anyamata a Saulo anali komweko, tsiku lija, anachedwetsedwa pamaso pa Yehova; dzina lake ndiye Doegi wa ku Edomu, kapitao wa abusa a Saulo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa