Levitiko 2:1 - Buku Lopatulika1 Ndipo munthu akabwera nacho chopereka ndicho nsembe yaufa ya kwa Yehova, chopereka chake chizikhala cha ufa wosalala; ndipo athirepo mafuta, ndi kuikapo lubani. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Ndipo munthu akabwera nacho chopereka ndicho nsembe yaufa ya kwa Yehova, chopereka chake chizikhala cha ufa wosalala; ndipo athirepo mafuta, ndi kuikapo lubani. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 “Munthu wina aliyense akabwera kudzapereka chopereka cha chakudya kwa Chauta, nsembeyo ikhale ya ufa wosalala. Ufawo authire mafuta ndi lubani, Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 “ ‘Munthu wina aliyense akabwera ndi nsembe ya chakudya kwa Yehova, chopereka chake chizikhala ufa wosalala. Ufawo ausakanize ndi mafuta ndi lubani, Onani mutuwo |
Ndipo iwo adzatenga abale anu onse mwa amitundu onse akhale nsembe ya kwa Yehova; adzabwera nao pa akavalo, ndi m'magaleta, ndi m'machila, ndi pa nyuru, ndi pa ngamira, kudza kuphiri langa lopatulika ku Yerusalemu, ati Yehova, monga ana a Israele abwera nazo nsembe zao m'chotengera chokonzeka kunyumba ya Yehova.