Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 1:17 - Buku Lopatulika

17 nang'ambe mapiko ake osawachotsa konse ai; ndipo wansembeyo aitenthe paguwa la nsembe, pa nkhuni zili pamoto; ndiyo nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 nang'ambe mapiko ake osawachotsa konse ai; ndipo wansembeyo aitenthe pa guwa la nsembe, pa nkhuni zili pamoto; ndiyo nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Pambuyo pake aing'ambe pakati, phiko lina uku, lina uku, koma osachotsa mapikowo. Kenaka aitenthe pa moto wankhuni wapaguwa. Imeneyo ndiyo nsembe yopsereza, yotentha pa moto, ya fungo lokomera Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Kenaka ayingʼambe pakati, koma asachotse mapiko. Ndipo wansembe ayiwotche pa nkhuni zimene zikuyaka pa guwa. Imeneyi ndi nsembe yopsereza, yowotcha pa moto ndiponso ya fungo lokomera Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 1:17
20 Mawu Ofanana  

Ndipo anatenga iye zonse zimenezo, nazidula pakati, naika bandu popenyana ndi linzake: koma mbalame sanazidule.


Ndipo Yehova anamva chonunkhira chakukondweretsa; nati Yehova m'mtima mwake, Sindidzatembereranso konse nthaka chifukwa cha munthu; pakuti ndingaliro ya mtima wa munthu ili yoipa kuyambira pa unyamata wake; sindidzaphanso konse zinthu zonse zamoyo, monga momwe ndachitiramo.


Pakuti simudzasiya moyo wanga kumanda; simudzalola wokondedwa wanu avunde.


Koma atsuke ndi madzi matumbo ndi miyendo; ndi wansembe abwere nazo zonse nazitenthe paguwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.


Ndipo abwere nayo kwa ana a Aroni, ansembewo; natengeko ufa, ndi mafuta odzala manja, ndi lubani wake wonse; ndipo wansembeyo aitenthe chikumbutso chake paguwa la nsembe, ndiyo nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.


Ndipo ana a Aroni azitenthe paguwa la nsembe, pa nsembe yopsereza, ili pa nkhuni zimene zili pamoto; ndiyo nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.


Ndipo adze nazo kwa wansembe, ndiye ayambe kubwera nayo ija ya kwa nsembe yauchimo, napotole mutu wake pakhosi pake, osauchotsa;


Ndipo chilamulo cha chopereka chaufa ndicho: ana a Aroni azibwera nacho pamaso pa Yehova ku guwa la nsembe.


Koma anatsuka matumbo ndi miyendo ndi madzi; ndi Mose anatentha mphongo yonse paguwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza yochita fungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.


Ndipo anapereka nsembe yopsereza kwa iye, chiwalochiwalo, ndi mutu wake; ndipo anazitentha paguwa la nsembe.


ndipo mukakonzera Yehova nsembe yamoto, nsembe yopsereza, kapena yophera, pochita chowinda cha padera, kapena nsembe yaufulu, kapena nsembe ya pa nyengo zanu zoikika, kumchitira Yehova fungo lokoma, la ng'ombe kapena nkhosa;


Ndi mwanawankhosa winayo umpereke madzulo; monga nsembe yaufa ya m'mawa, ndi nsembe yothira yake, umpereke; ndiyo nsembe yamoto ya fungo lokoma la Yehova.


Ndipo Yesu, pamene anafuula ndi mau aakulu, anapereka mzimu wake.


Pamene Yesu tsono adalandira vinyo wosasayo anati, Kwatha; ndipo anawerama mutu, napereka mzimu.


amene anaperekedwa chifukwa cha zolakwa zathu, naukitsidwa chifukwa cha kutiyesa ife olungama.


Pakuti Khristunso adamva zowawa kamodzi, chifukwa cha machimo, wolungama m'malo mwa osalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu; wophedwatu m'thupi, koma wopatsidwa moyo mumzimu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa