Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 2:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo abwere nayo kwa ana a Aroni, ansembewo; natengeko ufa, ndi mafuta odzala manja, ndi lubani wake wonse; ndipo wansembeyo aitenthe chikumbutso chake paguwa la nsembe, ndiyo nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo abwere nayo kwa ana a Aroni, ansembewo; natengeko ufa, ndi mafuta odzala manja, ndi lubani wake wonse; ndipo wansembeyo aitenthe chikumbutso chake pa guwa la nsembe, ndiyo nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 ndipo abwere nawo kwa ansembe, ana a Aroni. Atapeko ufa wosakaniza ndi mafuta uja dzanja limodzi, ndi lubani wake yense. Tsono wansembe atenthe zimenezo pa guwa, kusonyeza kuti nsembeyo yaperekedwa kwa Chauta, ndi nsembe yotentha pa moto, ya fungo lokomera Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 ndipo apite nawo kwa ansembe, ana a Aaroni. Atapeko modzazitsa dzanja ufa wosalala uja kuti ukhale wachikumbutso pamodzi ndi mafuta ndi lubani ndipo atenthe zonsezi pa guwa lansembe kuti zilandiridwe ndi Yehova mʼmalo mwa chopereka chonse. Iyi ndi nsembe yotentha pa moto ndiponso fungo lokomera Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 2:2
17 Mawu Ofanana  

Mundikumbukire Mulungu wanga mwa ichi, nimusafafanize zokoma zanga ndinazichitira nyumba ya Mulungu wanga, ndi maudikiro ake.


Ndipo ndinauza Alevi kuti adziyeretse, nabwere, nasunge pazipata kupatula tsiku la Sabata. Mundikumbukire ichinso, Mulungu wanga, ndi kundileka monga mwa chifundo chanu chachikulu.


Ndipo uzilandira ndalama za choteteza kwa ana a Israele, ndi kuzipereka pa ntchito ya chihema chokomanako; kuti zikhale chikumbutso cha ana a Israele pamaso pa Yehova, kuchita choteteza cha miyoyo yanu.


Wakupha ng'ombe alingana ndi wakupha munthu; iye wapereka nsembe ya mwanawankhosa alingana ndi wothyola khosi la galu; wothira nsembe yaufa akunga wothira mwazi wa nkhumba; wofukiza lubani akunga wodalitsa fano; inde iwo asankha njira zaozao, ndipo moyo wao ukondwerera m'zonyansa zao;


Koma atsuke ndi madzi matumbo ndi miyendo; ndi wansembe abwere nazo zonse nazitenthe paguwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.


nang'ambe mapiko ake osawachotsa konse ai; ndipo wansembeyo aitenthe paguwa la nsembe, pa nkhuni zili pamoto; ndiyo nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.


koma atsuke ndi madzi matumbo ake ndi miyendo yake; ndi wansembe atenthe zonsezi paguwa la nsembe, zikhale nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.


Ndipo wansembe atenthe chikumbutso chake, atatapa pa tirigu wake wokonola, ndi pa mafuta ake, ndi kutenga lubani lake lonse; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova.


Ndipo wansembeyo atengeko chikumbutso pa nsembe yaufa, nachitenthe paguwa la nsembe; ndicho nsembe yamoto ya fungo lokoma la kwa Yehova.


Nuike lubani loona ku mzere uliwonse, kuti likhale kumkate ngati chokumbutsa, nsembe yamoto ya Yehova.


Nachotse mafuta ake onse, monga umo amachotsera mafuta pa nsembe yoyamika; ndipo wansembeyo awatenthe paguwa la nsembe akhale fungo lokoma la kwa Yehova; ndi wansembe amchitire chomtetezera, ndipo adzakhululukidwa.


Koma chuma chake chikapanda kufikira njiwa ziwiri kapena maunda awiri, wochimwayo azidza nacho chopereka chake limodzi la magawo khumi la efa la ufa wosalala, likhale la nsembe yauchimo; asamaikapo mafuta, kapena kuikapo lubani ai; pakuti ndicho nsembe yauchimo.


Ndipo adze nacho kwa wansembe, ndi wansembeyo atengeko wodzala manja ukhale chikumbutso chake, nachitenthe paguwa la nsembe monga umo amachitira nsembe zamoto za Yehova; ndiyo nsembe yauchimo.


Ndipo atengeko wodzala manja pa ufa wa chopereka cha ufa wosalala, ndi pa mafuta ake, ndi lubani lonse lili pa chopereka chaufa, nazitenthe paguwa la nsembe, zichite fungo lokoma, ndizo chikumbutso chake cha kwa Yehova.


Pamenepo wansembeyo aike mkaziyo pamaso pa Yehova, navula mutu wa mkaziyo, naike nsembe yaufa yachikumbutso m'manja mwake, ndiyo nsembe yaufa yansanje; ndipo m'manja mwake mwa wansembe muzikhala madzi owawa akudzetsa temberero.


Wansembe atengekonso nsembe yaufa wodzala manja, chikumbutso chake, nachitenthe paguwa la nsembe; ndipo atatero amwetse mkazi madziwo.


Ndipo pompenyetsetsa iye ndi kuopa, anati, Nchiyani, Mbuye? Ndipo anati kwa iye, Mapemphero ako ndi zachifundo zako zinakwera zikhala chikumbutso pamaso pa Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa